1Bwanji ukunyadira ntchito zako zoipa,
munthu wamphamvuwe?
2Tsiku lonse umakhalira kusinkhasinkha za kuwononga ena,
lilime lako lili ngati lumo lakuthwa,
ntchito yako nkunyenga.
3Umakonda zoipa kupambana zabwino,
umakonda kunama kupambana kulankhula zoona.
4Umakonda kulankhula mau ovutitsa ena,
iwe wabodzawe.
5Koma Mulungu adzakutswanya kosalekeza,
adzakugwira ndi kukutulutsira kunja kwa nyumba yako.
Adzakuzula m'dziko la anthu amoyo.
6Anthu ochita zachilungamo adzaona zimenezi,
ndipo adzachita mantha.
Adzakuseka ndi kumanena kuti,
7“Muwoneni munthu amene sadafune kudalira Mulungu,
koma adakhulupirira chuma chake chochuluka,
nalimbikira kuchita zoipa.”
8Koma ine ndili ngati mtengo wauŵisi wa olivi
m'Nyumba ya Mulungu.
Ndimaika mtima nthaŵi zonse
pa chikondi chosasinthika cha Mulungu.
9Ndidzakuthokozani Inu Mulungu mpaka muyaya,
chifukwa cha zimene mwachita.
Ndidzatamanda dzina lanu pamaso pa anthu okukondani,
pakuti ndinu abwino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.