1Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu,
Israele anene choncho tsopano,
2Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu,
pamene anthu adatiwukira,
3bwenzi atatimeza amoyo,
muja mkwiyo wao udatiyakira,
4bwenzi chigumula chitatisesa,
madzi amkokomo atatikokolola,
5bwenzi madzi amphamvu atatimiza.
6Atamandike Chauta,
amene sadatipereke kwa anthuwo kuti atiwononge.
7Taonjoka ngati mbalame
mu msampha wa osaka,
msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka.
8Chithandizo chathu chimachokera kwa Chauta,
amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.