Lun. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mzimu wanu wosafa umakhala m'zinthu zonse.

2Nchifukwa chake anthu akakunyozani,

mumaŵalanga pang'onopang'ono.

Mumaŵakumbutsa machimo ao ndi kuŵachenjeza

kuti asiye zoipa ndi kukhulupirira Inu, Ambuye.

Mulungu alanga Akanani

3 Deut. 12.31; 18.9-13 Anthu akale amene ankakhala m'dziko lanu loyera

4mudadana nawo chifukwa cha zochita zao zonyansa,

chifukwa cha zaufiti ndi miyambo ina yoipa.

5Ankapha ana mopanda chifundo,

pa maphwando ao a nsembe zao

ankadya nyama ya anthu

ndi kumamwa magazi ao.

Adaphunzitsidwa miyambo yonyansadi,

6anakubala ankapha ana opanda chitetezo.

Inuyo mudagamula zoti makolo athu

aononge anthu amenewo,

7kuti dziko limene munkalikonda

kupambana maiko onse,

lilandire fuko loyenera la ana a Mulungu.

8 Eks. 23.28 Komabe popeza kuti adaniwo anali anthu,

mudaŵachitira chifundo.

Ankhondo anu asanafike,

mudatsogoza mavu ambiri

kuti akaononge adaniwo pang'onopang'ono.

9Kunali kotheka kwa Inu kuwononga anthu osamverawo

pakuŵayambanitsa nkhondo ndi anthu olungama,

kapena kuŵatsiriza onse kamodzinkamodzi ndi zilombo,

kapenanso ndi mau anu amodzi okha mopanda chisoni.

10 2Es. 9.11 Koma poŵalanga pang'onopang'ono,

mudaŵapatsa mpata wolapira,

chifukwa munkadziŵa bwino

kuti adabadwa m'machimo.

Kuipa kwao kunali kwachibadwa,

ndipo maganizo ao anali osasinthika.

11Unali mtundu wotembereredwa chiyambire.

Ngakhale mudaaŵalekerera machimo ao osaŵalanga,

sichinali chifukwa choopa wina aliyense ai.

Mulungu ndi wamphamvuzonse

12Ndani angakufunseni kuti,

“Kodi mwachita chiyani?”

Ndani angatsutsepo pa zogamula zanu?

Ndani angakuimbeni mlandu

chifukwa choti mwaononga mitundu ya anthu

imene inu nomwe mudailenga?

Ndani angabwere pamaso panu

kudzaŵalankhulira mau oteteza anthu osamveraŵa?

13Pajatu Mulungu ndinu nokha, palibenso wina.

Ndinu nokha amene mumasamala anthu onse.

Palibenso wina amene muyenera kumufotokozera

ngati chigamulo chanu ndi cholungama.

14Palibenso mfumu kapena muweruzi wina

amene angathe kukudzudzulani

pa za anthu amene mudaŵalanga.

15Ndinu olungama,

mumayendetsa zinthu zonse molungama.

Kwa Inu sizikugwirizana konse ndi mphamvu zanu

kuti mulange munthu wosayenera kulangidwa.

16Mphamvu zanu ndiye gwero la chilungamo chanu,

choncho popeza kuti ndinu mwini anthu onse,

mumaŵachitira chifundo onse.

17Anthu amene amakayika

kuti ndinu Mulungu Wamphamvuzonse,

mumaŵaonetsa mphamvu zanu.

Anthu amene amadziŵa zimenezi

nkukuchitanibe chipongwe,

mumaŵachititsa manyazi.

18Koma ngakhale ndinu mwini mphamvu,

mumaweruza mofatsa.

Mumatilamula ndi mtima wachifundo,

poti mukangofuna,

mumaonetsa mphamvu zanu.

Mulungu atiwonetsa phindu la kupirira

19Pochita ntchito zanu zoterezi,

mudaphunzitsa anthu anu kuti wolungama ayenera

kukhala wachifundo,

mudadzaza ana anu ndi chikhulupiriro,

chifukwa mumakhululukira anthu ochimwa.

20Ngati adani a ana anu mudaŵalanga mofatsa

ndi moleza mtima,

ngakhale ankayenera kuphedwa,

mudaŵapatsa nthaŵi yosiya machimo ao pakutero,

21nanji tsono ana anu,

iwowo mudaŵaweruza mosamala kopambana,

Inu amene mudapereka kwa makolo ao

malonjezo anu ndi chipangano chanu

kuti mudzaŵapatsa madalitso ochuluka.

22Ife mukamatilanga,

adani mumaŵasautsa moŵirikiza,

kuti tizilingalira bwino za chifundo chanu

pamene tikuweruza ena,

kuti Inu podzatiweruza,

tidzathe kudalira chifundo chanu.

Mulungu alanga Aejipito

23Tsono anthu openga aja,

amene anali ndi makhalidwe oipa,

mudaŵalanga ndi zoipa zao zomwe.

24Iwo adasokera kwambiri ndi njira zao zonama,

kotero kuti nyama zoipa ndi zonyansa kwambiri

ankaziyesa milungu.

Ankangokhulupirira zopusa

ngati ana opanda nzeru.

25Nchifukwa chake iwowo

pokhala ngati ana opanda nzeru,

mudaŵatumizira chilango chanu

choŵaonetsa kuti ndi opusa.

26Koma amene sadasamaleko madzudzulo ochenjezawo,

adzalandira chilango choyenera kwa Mulungu.

27Mutaŵalanga nazo zolengedwa

zimene adaaziyesa milungu zija,

adapsa nazo mtima zoŵazunzazo.

Adaona ndi kuzindikira kuti

Chauta ndiye Mulungu woona,

Iye amene iwo adaakana kumuvomera.

Nchifukwa chake chilango choopsa chidaaŵagwera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help