1Benjamini adabereka Bela mwana wake wachisamba, Asibele mwana wake wachiŵiri, Ahara mwana wake wachitatu,
2Noha mwana wake wachinai ndi Rafa mwana wake wachisanu.
3Bela anali ndi zidzukulu izi: Adara, Gera, Abihudi,
4Abisuwa, Namani, Ahowa,
5Gera, Sefufani ndiponso Huramu.
6Ana a Ehudi amene anali atsogoleri a mabanja okhala ku Geba, adachotsedwa kwaoko ndipo adakakhala ku Manahati.
7Anawo anali Namani, Ahiya ndi Gera. Gerayo amene anali bambo wake wa Uza ndi Ahihudi, ndiye adatsogolera anthu osamutsidwawo.
8Saharaimu, atachotsa akazi ake Husimu ndi Baara, adakhala ndi ana m'dziko la Mowabu.
9Mwa mkazi wake Hodesi adabelekamo ana aŵa: Yobabu, Zibiya, Mesa, Malikamu,
10Yeuzi, Sakiya ndi Mirima. Ameneŵa ndiwo amene anali ana ake, atsogoleri a mabanja.
11Mwa Husimu adaberekamonso ana aŵa: Abitubu, ndi Elipaala.
12Ana a Elipaala naŵa: Ebere, Misamu ndi Semedi. Semedi ndiye adamanga mizinda ya Ono ndi Lodi pamodzi ndi midzi yake yomwe.
Abenjamini ku Gati ndi ku Aiyaloni13Beriya ndi Sema anali atsogoleri a mabanja okhala ku mzinda wa Aiyaloni. Iwowo adathaŵitsa nzika za ku Gati.
14Zidzukulu zina za Beriya zinali Ahiyo, Sasaki, Yeremoti,
15Zebadiya, Aradi, Edere,
16Mikaele, Isipa ndi Yoha.
Abenjamini ku Yerusalemu17Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Hebere,
18Isimerai, Iziliya ndi Yobabu anali zidzukulu za Elipaala.
19Yakimu, Zikiri, Zabidi,
20Eliyenai, Ziletai, Eliyele,
21Adaya, Beraya ndi Simiratu anali zidzukulu za Simei.
22Isipani, Ebere, Eliyele,
23Abidoni, Zikiri, Hanani,
24Hananiya, Elamu, Anitotiya,
25Ifidea ndi Penuwele, anali zidzukulu za Sasaki.
26Samuserai, Sehariya, Ataliya,
27Yaaresiya, Eliya ndi Zikiri anali zidzukulu za Yerohamu.
28Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mabanja, anthu otchuka potsata mibadwo yao, ndipo onsewo ankakhala ku Yerusalemu.
Abenjamini ku Gibiyoni ndi ku Yerusalemu29Yeiyele, amene adaamanga Gibiyoni, ankakhala ku Gibiyoni komweko. Mkazi wake anali Maaka.
30Mwana wake wachisamba anali Abidoni, pambuyo pa iyeyo panali Zuri, Kisi, Baala, Nere, Nadabu,
31Gedori, Ahiyo, Zekeri,
32ndi Mikiloti bambo wa Simea). Tsono, monga achibale ao aja, iwoŵanso ankakhala ku Yerusalemu pamodzi ndi achibale aowo.
Banja la mfumu Saulo33Nere adabereka Kisi, Kisi adabereka Mfumu Saulo, Mfumu Saulo adabereka Yonatani, Malikisuwa, Abinadabu, ndi Esibaala.
34Yonatani adabereka Meribaala. Meribaala adabereka Mika.
35Ana a Mika naŵa: Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi.
36Ahazi adabereka Yehoyada, Yehoyada adabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimiri. Zimiri adabereka Moza,
37Moza adabereka Bineya, Bineya adabereka Rafa, Rafa adabereka Eleasa, Eleasa adabereka Azele.
38Azele anali ndi ana asanu ndi mmodzi, ndipo maina ao naŵa: Azirikamu, Bokeru, Ismaele, Seyariya, Obadiya ndi Hanani. Onseŵa anali ana a Azele.
39Ana a mbale wake Eseki naŵa: mwana wake wachisamba Ulamu, wachiŵiri Yeusi, wachitatu Elifeleti.
40Ana a Ulamu anali ankhondo amphamvu, anthu amauta, ndipo anali ndi ana ndi adzikulu 150. Onseŵa anali Abenjamini.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.