Yob. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Apo Yobe adayankha kuti,

2“Leronso ndikudandaula kwambiri kwa Mulungu.

Ngakhale ndikubuula,

Mulungu akundilangiralangira ndithu.

3Ha, ndikadadziŵa kumene ndikadampeza Mulungu,

kuti ndikafike mpaka komwe amakhalako!

4Ndikadakamba mlandu wanga pamaso pake,

bwenzi nditafotokoza zifukwa zanga zonse.

5Bwenzi nditamva mau amene akadandiyankha,

bwenzi nditamvetsa zimene akadandiwuza.

6Kodi Mulungu akadalimbana nane ndi mphamvu zake?

Ai, koma akadamva mau anga.

7Kumeneko munthu wolungama

akadalankhula ndi Iye modekha.

Wondiweruzayo akadandipeza wosalakwa nthaŵi zonse.

8“Taonani, ndikapita chakutsogolo,

Iye kulibe kumeneko,

ndikabwerera cham'mbuyo, sinditha kumupenya.

9Ndimamfunafuna kumanzere, koma osamuwona.

Ndimayang'ananso kumanja, koma osampenya ndithu.

10Komabe Mulungu amadziŵa m'mene ndimayendera,

akandiyesa adzapeza kuti ndine wangwiro ngati golide.

11Mapazi anga akuponda m'mapazi mwake,

ndasunga njira yake, ndipo sindidaitaye.

12Sindidapatuke kusiya malamulo ake.

Ndasunga mau a pakamwa pake

kupambana zofuna zanga zonse.

13“Iyeyo ndi wosasinthika,

nanga ndani angathe kumsintha maganizo?

Zimene wafuna, amazichitadi.

14Zimene adatsimikiza kuti adzandichita, adzachitadi,

ndipo amalingalira zambiri zoterezi.

15Nchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri

pamaso pake.

Ndikaganiza za iyeyo, ndimaopa kwabasi.

16Mulungu walefula mtima wanga.

Mphambe wandiwopsa.

17Wandichititsa mantha ndi Mulungu,

osati mdima wa mavuto onse amene amandiphimbaŵa.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help