1Yudasi anali atamva mbiri ya Aroma, kuti anali ndi ankhondo amphamvu kwambiri, ndipo kuti ankachitira chifundo onse ofuna kuyanjana nawo. Adaamvanso kuti Aromawo ankapalana chibwenzi ndi munthu aliyense wodza kwa iwo.
2Adaamva kuti ngamphamvu kwambiri. Anthu adamsimbira za nkhondo zao zoonetsa kulimba mtima, zimene adaazichita pakati pa Agolo, m'mene adaŵagonjetsera nkumaŵakhometsa msonkho.
3Adaamvanso zonse zimene adaazichita ku Sipeni, monga pamene adalanda migodi ya siliva ndi golide yokhala kumeneko.
4Adamvanso kuti Aromawo, chifukwa cha nzeru zao ndi khama lao adaagonjetsa dziko lonselo ngakhale nkutali ndi kwao. Chimodzimodzi mafumu amene adaabwera kuchokera ku malekezero a dziko lapansi kudzachita nawo nkhondo, Aromawo adaŵagonjetsa nkuŵaonongeratu, ndipo otsala mwa iwo ankaŵakhometsa msonkho chaka chilichonse.
5Panalinso Filipo ndi Perseyo mfumu ya ku Kitimu ndi anzao enanso, amene adaaukira Aroma kuti achite nawo nkhondo. Onsewo adaŵathyola nkuŵagonjetsa.
6Antioko wamkulu, mfumu ya ku Asiya, amene adadzamenya nawo nkhondo atatenga njovu 120 ndi ankhondo a pa akavalo ndi am'magaleta, pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo, nayenso adamgonjetsa.
7Adamgwira wamoyo, namuumiriza iyeyo ndi odzaloŵa ufumu wake kupereka msonkho waukulu, kuperekanso anthu kuti akhale ngati zikole. Kenaka adamlanda madera ena abwino koposa m'dziko lakelo,
8monga Indiya, Mediya ndi Lidiya, naŵapereka kwa mfumu Eumenesi.
9Agriki nawonso adaaganiza zoononga Aroma. Iwowo atamva,
10adatuma mtsogoleri wamkulu mmodzi yekha wa asilikali. Iyeyo adamenyana nawo nkhondo, napha anthu ambiri. Adatenga akazi ao ndi ana ao kunka nawo ku ukapolo. Adalanda chuma chao, adagonjetsa dziko lao nkugumula nyumba zao zankhondo. Adaŵasandutsa akapolo mpaka lero lino.
11Anthu a maiko ena onse ndi a ku zilumba zonse amene adalimbana nawo, adaŵafilifita nkuŵasandutsa akapolo.
12Koma abwenzi ao, ndi onse oŵadalira, akhala akusunga bwino chibwenzicho. Akhala akugonjetsa mafumu akufupi ndi kwao ndi akutali omwe, motero anthu onse omva mbiri yao akuchita nawo mantha.
13Onse amene Aroma atsimikiza kuŵathandiza kuti akhale mafumu, akhaladi mafumu, ndipo amachotsa mfumu pa mpando wake monga afunira. Mphamvu zao ndi ulamuliro wao zinali zodziŵika pa dziko lonse lapansi.
14Komabe pakati paopo palibe ndi mmodzi yemwe amene adavalapo chisoti chaufumu, kapena zovala zofiirira kuwonetsa kupambana anzake.
15Adadzipangira bungwe lapamwamba la akuluakulu 320. Anthu ameneŵa tsiku ndi tsiku amakambirana zokhudza anthu ao, m'mene angaŵasamalire bwino.
16Chaka chilichonse amapatsa mphamvu kwa munthu mmodzi yekha kuti azilamulira ndi kuyendetsa dziko lonse. Onse amamumvera mmodzi yekhayo, ndipo palibe wochita kaduka kapena nsanje.
Kugwirizana pakati pa Ayuda ndi Aroma17 2Am. 4.11 Yudasi adasankhula Eupoleme, mwana wa Yohane wa m'banja la Akosi, ndi Yasoni mwana wa Eleazara, naŵatuma ku Roma kuti akachite nawo chipangano cha chibwenzi ndi chiyanjano.
18Adafunanso kuti aŵachotsere goli loŵalemera, chifukwa adaaona kuti Agriki ankazunza Aisraele ndi ukapolo.
19Tsono aŵiriwo adapitadi ku Roma, ndipo ulendo wao unali wa masiku ambiri. Ataloŵa m'bungwe la akuluakulu lija adanena mau ao, adati,
20“Yudasi Makabeo ndi abale ake, pamodzi ndi Ayuda onse, atituma kwa inu kuti tidzachite nanu chipangano cha chiyanjano ndi cha mtendere, ndipo kuti mutilembe pamodzi ndi anthu oyanjana nanu ndi abwenzi anu.”
21Mauwo adaŵakomera akuluakuluwo.
221Am. 14.18Tsono naŵa mau amene Aroma adaŵalemba pa mabandu amkuŵa, naŵatumiza ku Yerusalemu, kuti akhale mboni ya mtendere ndi chiyanjano kwa Ayuda.
23Adalemba kuti, “Aroma ndi Ayuda azikhazikana mwamtendere nthaŵi zonse pa nyanja ndi pa mtunda! Nkhondo iŵakhalire kutali, ndiponso adani asaŵayandikire.
24Akatsogola ndi Aroma kukhala pa nkhondo, kapena abwenzi ao, kapena aliyense wokhala mu ulamuliro wao wonse,
25gulu la Ayuda lidzaŵathandiza ndi mtima wonse, monga m'mene zidzathekere nthaŵi imeneyo.
26Asadzapereke tirigu, zida, ndalama kapena zombo kwa adani a Aroma, potsata malamulo a Aroma. Ndipo Ayuda adzasunga malonjezo aowo osalandirapo kanthu.
27Momwemonso akayamba ndi Ayuda kukhala pa nkhondo, Aroma adzamenya nkhondo pamodzi nawo, monga m'mene zidzathekere nthaŵi imeneyo.
28Aroma sadzapatsa ogwirizana ndi adani a Ayuda tirigu, zida, ndalama kapena zombo, potsata malamulo a Aroma. Ndipo Aroma adzasunga malonjezo ao mosanyenga konse.
29Ameneŵa ndiwo mau a chipangano chimene Aroma akuchita ndi Ayuda.
30Ngati pambuyo pake Aroma ndi Ayuda afuna kuwonjezapo pa mauwo, kapena kuchotsapo mau ena, adzachita zimenezo mwaufulu, ndipo zilizonse zimene adzaonjeze kapena kuchotsa adzazitsata ngati chipangano chimene.
31“Kunena za zovuta zimene mfumu Demetriyo adaŵachita Ayuda, tamulembera iyeyo mau aŵa akuti, ‘Chifukwa chiyani ukuŵathyola khosi Ayuda ndi goli lako, pamene iwowo ndi abwenzi athu oyanjana nafe?
32Akatidandauliranso pa zochita zako, tidzaŵathandiza monga kuyenera, ndipo tidzachita nawe nkhondo pa nyanja ndi pa mtunda.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.