1Kodi mumagamuladi molungama,
inu akuluakulu oweruza?
Kodi mumaweruzadi anthu mwachilungamo?
2Iyai, mitima yanu imangolingalira zoipa,
kuweruza kwanu kosalungama kumadzetsa chiwawa.
3Anthu oipa ndi osokera
kuyambira ali m'mimba mwa mai ao,
anthu amabodza ndi otayika
kuyambira tsiku la kubadwa kwao.
4Ali ndi ululu wonga wa njoka,
ali ngati mphiri yogontha,
imene yatseka makutu ake,
5kotero kuti siimva liwu loitana la kamatsenga,
ngakhale akhale wochenjera chotani.
6Inu Mulungu, gululani mano a m'kamwa mwao,
phwanyani nsagwada za mikangoyi, Inu Chauta.
7Azimirire ngati madzi opita,
mivi yao iŵafotere m'manja ngati udzu.
8Akhale ngati nkhonodambe imene imazimirira poyenda,
ngati mtayo wosaona dzuŵa.
9Miphika yanu isanagwire moto wa nkhuni zaminga,
zingakhale zaziŵisi kapena zoyaka,
Mulungu aziseseretu nkuzichotsa.
10Munthu wangwiro adzakondwera poona kulipsirako.
Adzasamba mapazi ake m'magazi a anthu oipawo.
11Motero anthu adzati,
“Zoona, olungama amalandiradi mphotho.
Alipodi Mulungu amene amaweruza pa dziko lapansi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.