Yos. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Dziko limene Efuremu ndi Manase wakuzambwe adalandira.

1Dziko limene lidapatsidwa kwa zidzukulu za Yosefe lidayambira ku mtsinje wa Yordani pafupi ndi Yeriko, cha kuvuma kwa akasupe a Yeriko, kukaloŵa m'chipululu. Lidayambiranso ku Yeriko, ndi kukaloŵa m'dziko lamapiri chakuzambwe, mpaka kukafika ku chipululu cha Betele.

2Kuchokera ku Betele malire ake adakafika ku Luzi, nabzola ku Ataroti kumene kunkakhala Aaraki.

3Tsono lidapitirira ndithu kuzambwe, kudera la Ayafaleti, mpaka kufika kunsi kwa Betehoroni. Kuchokera kumeneko malire ake adalunjika ku Gezere, nakalekeza mpaka ku nyanja.

4Choncho ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu adalandira choloŵa chao.

Dziko la Efuremu.

5Dziko la mabanja a Efuremu ndi ili: malire ake akuvuma anali Ataroti-Adara mpaka kukafika kumtunda kwake kwa Betehoroni.

6Kuchokera kumeneko malirewo adatsikira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuvuma malirewo adakhotera cha ku Taanatisilo, napitirira malo amenewo chakuvuma, mpaka kukafika ku Yanowa.

7Tsono kuchokera ku Yanowa, adatsikira ku Ataroti ndi ku Naara. Adakafika ku Yeriko ndi kukathera m'Yordani.

8Malirewo adaloŵera kuzambwe kuchokera ku Tapuwa mpaka ku mtsinje wa Kana, ndi kutsikira mpaka ku nyanja. Dziko limenelo ndilo lidapatsidwa kwa mabanja a Aefuremu kuti likhale choloŵa chao,

9kuphatikizapo mizinda ndi midzi yopatsidwa kwa Aefuremu, koma yokhala m'kati mwa dziko la anthu a fuko la Manase.

10Owe. 1.29 Komatu Akanani amene ankakhala ku Gezere, Aefuremu sadaŵapirikitse, kotero kuti Akanani ameneŵa alipobe pakati pa Aefuremu mpaka lero lino. Komabe Akananiwo ankakakamizidwa kugwira ntchito yathangata.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help