Miy. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Malangizo ena a Solomoni.

1Enanso ndi aŵa malangizo a Solomoni amene anthu a Hezekiya, mfumu ya ku Yuda adaŵalemba:

2Ulemerero wa Mulungu wagona pa kubisa zinthu,

m'menemo ulemerero wa mafumu wagona

pa kuzifufuza zinthuzo.

3Monga momwe uliri mlengalenga kutalika,

ndi momwe liliri dziko lapansi kuzama,

ndi m'mene aliri maganizo a mfumu kusadziŵika kwake.

4Chotsa zoipa m'siliva,

ndipo wosula adzatha kupanga naye chiŵiya.

5Muchotse aphungu oipa pamaso pa mfumu,

ndipo ufumu wake udzakhazikika pa chilungamo.

6 Lk. 14.8-10 Usamadzikuza ukakhala pamaso pa mfumu,

usamakhala pa malo a anthu apamwamba.

7Pajatu kuli bwino kuchita kukuuza kuti,

“Dzakhale pokwera pano”, koposa kuchita kukutsitsa

chifukwa cha wina wokupambana.

Zimene maso ako azipenya,

8usafulumire kupita nazo ku bwalo lamilandu,

chifukwa udzatani nanga pambuyo pake,

ngati mnzako akuchititsa manyazi pokutsutsa?

9Mnzako uzichita kukamba naye zinthu,

ndipo usaulule chinsinsi cha wina,

10kuwopa kuti wina akamva mau ako,

angakuchititse manyazi, ndipo mbiri yako yoipa sidzatha.

11Mau amodzi olankhula moyenera

ali ngati zokongoletsera zagolide m'choikamo chasiliva.

12Kwa munthu womvetsera bwino,

kudzudzula kuli ngati mphete yagolide,

kapena chokongoletsera china chagolide.

13Kwa anthu amene amtuma,

wamthenga wokhulupirika ali ngati madzi ozizira

pa nthaŵi yotentha, amaziziritsa mtima wa mbuyake.

14Munthu wonyadira mphatso imene saipereka,

ali ngati mitambo ndi mphepo zopanda mvula.

15Kupirira ndiye kumagonjetsa wolamula,

ndipo kufeŵa m'kamwa kumafatsitsa mtima wouma.

16Ukapeza uchi, ingodya wokukwanira,

kuwopa kuti ungakoledwe nawo nkuyamba kusanza.

17Kunyumba kwa mnzako uzipitako kamodzikamodzi,

kuwopa kuti angatope nawe, nkuyamba kudana nawe.

18Munthu wochitira mnzake umboni wonama,

amapweteka mnzakeyo ngati chibonga kapena

lupanga kapena muvi wakuthwa.

19Kukhulupirira munthu wosakhulupirika

pa nthaŵi yamavuto

kuli ngati kudya ndi dzino loŵaŵa,

kapena kuyenda ndi mwendo wothyoka.

20Kuimbira nyimbo munthu wachisoni

kuli ngati kumvula zovala pa nyengo yachisanu,

ndiponso ngati kumthira vinyo wosasa pa chilonda.

21 Aro. 12.20 Mdani wako akakhala ndi njala, umpatse chakudya,

akamva ludzu, umpatse madzi akumwa.

22Potero udzamchititsa manyazi aakulu,

ndipo Chauta adzakupatsa mphotho.

23Mphepo ya mpoto ndiyo imadza ndi mvula,

chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.

24Kuli bwino kukhala potero pa denga,

kupambana kukhala m'nyumba

pamodzi ndi mkazi wolongolola.

25Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali

uli ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.

26Munthu wabwino amene amagonjera munthu

woipa amafanafana ndi kasupe wodzaza ndi matope

kapena chitsime cha madzi oipa.

27Si kwabwino kudya uchi wambiri,

tsono muchenjere nawo mau oyamikira.

28Munthu wosadzimanga mtima

ali ngati mzinda umene adani authyola

nkuusiya wopanda malinga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help