Eks. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chauta adauza Moseyo kuti, “Uwona tsopano zimene ndimchite Farao. Ndidzakakamiza Farao kuti atulutse anthu anga m'dziko lake. Ndithudi, adzaŵatulutsiratu m'dzikomo, chifukwa ndidzamkakamiza ndi dzanja langa lamphamvu. Zoonadi, dzanja langa lamphamvu lidzamuumiriza kuti aŵapirikitse.”

Mulungu aitana Mose

2

3Ndidaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobe ngati Mulungu Mphambe, koma sindidaŵadziŵitse dzina langa kuti ndine Chauta.

4Ndidachita nawo chipangano ndi kuŵalonjeza kuti ndidzaŵapatsa dziko la Kanani, momwe adakhalamo kale ngati alendo.

5Tsopano ndamva kudandaula kwa Aisraele, amene ali mu ukapolo wa Aejipito, ndipo ndakumbukira chipangano changa.

6Tsono iwe ukaŵauze Aisraele mau anga oti, ‘Ine ndine Chauta. Ndidzakutulutsani mu ukapolo wa ntchito yakalavulagaga imene Aejipito akukukakamizani kuigwira. Ndidzakupulumutsani ndi dzanja langa lotambalitsa ndiponso pochita ntchito zamphamvu.

7Inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Mudzazindikira kuti ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakupulumutsani ku ntchito yakalavulagaga imene Aejipito akukukakamizani kuigwira.

8Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanulanu. Ine ndine Chauta.’ ”

9Mose adauza Aisraele zimenezi, koma iwo sadamvere, chifukwa choti anali atataya kale mtima, pomakhala mu ukapolo wao mwankhalwe chotere.

10Tsono Chauta adauza Mose kuti,

11“Pita kamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.”

12Koma Mose adauza Chauta kuti, “Ngati Aisraele enieniwo sandimvera ine, nanji Farao angandimvere bwanji? Inetu paja sindikhoza kulankhula bwino.”

13Koma Chauta adalamula Mose ndi Aroni kuti akauze Aisraele ndi Farao mfumu ya ku Ejipito, kuti Aisraelewo ayenera kutuluka m'dziko la Ejipito.

Mibadwo ya Mose ndi Aroni

14Naŵa atsogoleri a mabanja a makolo ao. Ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele, anali aŵa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Rubeni.

15Ana a Simeoni naŵa: Yemuwele, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo mwana wa kwa mkazi wa ku Kanani. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Simeoni.

16Num. 3.17-20; 26.57, 58; 1Mbi. 6.16-19 Maina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zao naŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Leviyo adakhala zaka 137 ali moyo.

17Ana a Geresoni naŵa: Libini ndi Simeyi pamodzi ndi mabanja ao.

18Ana a Kohati naŵa: Amuramu, Izihara, Hebroni ndi Uziyele. Kohati adakhala zaka 133 ali moyo.

19Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Ameneŵa ndiwo mabanja a Levi pamodzi ndi zidzukulu zao.

20Amuramu adakwatira mlongo wa bambo wake dzina lake Yokebede. Yokebedeyo adabala Aroni ndi Mose. Amuramu adakhala zaka 137 ali moyo.

21Ana a Izihara naŵa: Kora, Nefegi ndi Zikiri.

22Ana a Uziyele naŵa: Misaele, Elizafani ndi Sitiri.

23Aroni adakwatira Eliseba mwana wa Aminadabu, ndipo mlongo wake anali Nasoni. Eliseba adabala Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.

24Ana a Kora naŵa: Asiri, Elikana ndi Abiyasafu. Ameneŵa ndiwo mabanja a Kora.

25Eleazara mwana wa Aroni adakwatira mmodzi mwa ana a Putiyele, amene adamubalira Finehasi. Ameneŵa ndiwo atsogoleri a mabanja a Alevi malinga ndi mafuko ao.

26Mose ndi Aroni ndi omwe aja amene Chauta adaŵauza kuti, “Atulutseni Aisraele m'dziko la Ejipito mwa magulumagulu.”

27Ameneŵa ndiwo ankauza Farao mfumu ya ku Ejipito kuti atulutse Aisraele ku Ejipito.

Chauta alamula Mose ndi Aroni

28Pamene Chauta adalankhula ndi Mose ku dziko la Ejipito,

29adati “Ine ndine Chauta. Ukamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, zonse zimene ndikuuze.”

30Koma Mose adauza Chauta kuti, “Inu mukudziŵa kuti paja ndine wosakhoza kulankhula, nanga Faraoyo adzandimvera bwanji?”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help