1 Aro. 3.10-12 Mumtima mwake munthu wopusa amati,
“Kulibe Mulungu.”
Anthu otereŵa ndi oipa,
amachita zonyansa,
palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.
2Mulungu kumwambako waŵerama,
akuyang'ana anthu pansi pano,
kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru
wofunitsitsa Mulungu.
3Koma ai anthu onse ndi osokera,
onsewo ndi oipa chimodzimodzi.
Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino,
ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe.
4Kani anthu oipaŵa alibe nzeru chotere?
Iwo amameza anthu anga, kuŵayesa chakudya,
ndipo samutama Mulungu mopemba.
5Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu,
mantha ake amene sadaoneke ndi kale lonse.
Pakuti Mulungu adzaononga adani okuzingani.
Inu mudzaŵachititsa manyazi
chifukwa Mulungu waŵakana.
6Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele
kuchokera ku Ziyoni!
Mulungu akadzaŵabwezera ufulu anthu ake,
Yakobe adzakondwera,
Israele adzasangalala kwambiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.