1 Maf. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Eliya athaŵira ku phiri la Sinai

1Ahabu adauza Yezebele zonse zimene adachita Eliya zija, ndipo kuti adapha aneneri onse a Baala ndi lupanga.

2Pomwepo Yezebele adatuma munthu kukauza Eliya kuti, “Milungu indilange ngakhale kundipha kumene, ngati sindikupha iweyo maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, monga momwe udaphera aneneriwo.”

3Pamenepo Eliya adachita mantha, ndipo adanyamuka nathaŵa kuti apulumutse moyo wake. Adakafika ku Beereseba, mzinda wa ku Yuda, nakasiya mtumiki wake kumeneko.

4 Yon. 4.3 Koma Eliya mwini wake adayenda ulendo wa tsiku limodzi m'chipululu, nakakhala pansi patsinde pa kamtengo ka tsache. Tsono adapempha kuti afe, adati, “Zandikola! Inu Chauta, bwanji ndingofa basi! Ine sindingapambane makolo anga.”

5Atatero adagona tulo patsinde pa kamtengo ka tsache pomwepo. Mwadzidzidzi mngelo adamkhudza namuuza kuti, “Dzuka, udye.”

6Eliya atapenya, adangoona kuti kumutu kwake kuli buledi wootcha pa makala, ndiponso mkhate wa madzi. Adadya, namwera, nkugonanso.

7Mngelo wa Chauta uja adabweranso kachiŵiri, namkhudza nati, “Dzuka, udye kuti ulendowu ungakukanike.”

8Eliya uja adadzuka, nadya nkumwera. Motero adapeza mphamvu zoyendera. Adayenda masiku makumi anai usana ndi usiku mpaka adakafika ku Sinai, phiri la Mulungu.

9Kumeneko adafikira m'phanga, nagona momwemo. Tsono Chauta adadzamuuza kuti, “Ukuchitako chiyani kuno, iwe Eliya?”

10Aro. 11.3 Eliya adayankha kuti, “Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ineyo ndakhala ndikutumikira Inu nokha nthaŵi zonse. Koma anthu a ku Israele aphwanya chipangano chimene adachita ndi Inu, ndipo agwetsa maguwa anu ndi kupha aneneri anu ndi lupanga. Ineyo ndangotsala ndekha. Tsono akufunafunanso moyo wanga, kuti andiphe.”

11Apo Chauta adati, “Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga.” Tsono Chauta adadutsa pamenepo, ndipo mphepo yamphamvu idaomba ning'amba mapiri ndi kuswa matanthwe, koma Chauta sanali m'mphepomo. Itapita mphepoyo, padachita chivomezi, koma Chauta sanali m'chivomezimo.

12Chitapita chivomezi chija, padafika moto, koma Chauta sanali m'motomo. Utapita motowo, padamveka kamphepo kongoti wii.

13Eliya atakamva, adafunda kumutu, ndipo adatuluka, nakaima pa khomo la phanga. Pomwepo padamveka mau omuuza kuti, “Ukuchita chiyani kuno, iwe Eliya?”

14Iyeyo adati, “Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ineyo ndakhala ndikutumikira Inu nokha nthaŵi zonse. Koma anthu a ku Israele aphwanya chipangano chimene adachita ndi Inu, ndipo agwetsa maguwa anu ndi kupha aneneri anu ndi lupanga. Ineyo ndangotsala ndekha. Tsono akufunafunanso moyo wanga kuti andiphe.”

152Maf. 8.7-13 Apo Chauta adamuuza kuti, “Bwerera, tsata njira yopita ku chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaele kuti akhale mfumu ya ku Siriya.

162Maf. 9.1-6 Yehu mwana wa Nimisi ukamdzoze kuti akhale mfumu ya ku Israele. Ndipo Elisa, mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola, ukamdzoze kuti akhale mneneri woloŵa m'malo mwako.

17Tsono amene adzapulumuke ku lupanga la Hazaele, Yehu adzamupha. Amene adzapulumuke ku lupanga la Yehu, Elisa adzamupha.

18Aro. 11.4 Komabe ku Israele ndasungako anthu zikwi zisanu ndi ziŵiri, omwe sadagwadireko Baala kapena kumpsompsona fano lake.”

Chauta aitana Elisa

19Eliya atachoka kumeneko, adakapeza Elisa akulima ndi pulawo yokokedwa ndi ng'ombe. Panali magoli khumi ndi aŵiri, mwiniwakeyo nkumakuyenda ndi goli lotsiriza. Eliya adabwera kumene kunali iyeko, namuveka mwinjiro wake.

20Pomwepo Elisa adasiya ng'ombe zakezo, adathamangira Eliya uja nampempha kuti, “Mundilole kuti ndikatsazike bambo wanga ndi mai wanga, ndipo pambuyo pake ndidzakutsatani.”

21Eliya adamuyankha kuti, “Chabwino, pita. Ndakuletsa ngati?” Apo Elisa adabwerera, ndipo adatenga ng'ombe zake ziŵiri nazipha. Kenaka adatenga magoli a ng'ombezo nasonkhera moto nkuphikira nyamayo, ndipo adaipereka kwa anthu kuti adye. Pambuyo pake adanyamuka namayenda ndi Eliya ndi kumamtumikira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help