1 kapena maguwa ofukizapo lubani.
9Tsiku limenelo mizinda yamphamvu ya Aisraele idzasiyidwa monga mizinda ya Aamori ndi ya Ahivi imene anthu adaaisiya pothaŵa Aisraelewo. Ndipo idzakhala mabwinja.
10Inu Aisraele, mwaiŵala Mulungu Mpulumutsi wanu,
simudamkumbukire Iye
amene ndiye thanthwe lokupulumutsani.
M'malo mwake, mumabzala mbeu zabwino,
kubzalira milungu yachilendo,
11Mumati zikule tsiku lomwe mwabzalalo,
mumati zituluke maluŵa m'maŵa momwe mwazibzalamo,
komabe zimene mudzakololezo
zidzatha pa tsiku lamavuto,
ndipo mazunzo ake adzakhala osatha.
Adani agonjetsedwa12Ha, anthu a mitundu yambiri
akusokosa kwambiri!
Phokoso lao lili ngati kukokoma kwa nyanja!
Ha, lumbwe la anthu a mitundu ina,
likusokosa ngati madzi amphamvu!
13Ankhondo a mitundu ina akubwera
ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri.
Koma Mulungu akuŵadzudzula,
ndipo iwo adzathaŵira kutali.
Adzapirikitsidwa ngati mankhusu
ouluka ndi mphepo pa mapiri,
ngati fumbi la kamvulumvulu namondwe asanayambe.
14Pa nthaŵi yamadzulo ndi oopsa!
Koma kusanache, onse azimirira.
Umu ndimo m'mene zidzaŵachitire
anthu otilanda zathu.
Limeneli ndilo tsoka la anthu otibera zinthu zathu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.