Neh. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nehemiya adera nkhaŵa Yerusalemu

1Naŵa mau a Nehemiya, mwana wa Hakaliya:

Pa mwezi wa Kisilevi, chaka cha 20 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, pamene ndinali mu mzinda wa Susa,

2Hanani, mmodzi mwa abale anga, adabwera ndi anthu ena kuchokera ku Yuda. Ndipo ndidaŵafunsa za Yerusalemu ndiponso za Ayuda amene adaatsalirako osatengedwa ukapolo.

3Adandiyankha kuti, “Anthu amene aja ali pa mavuto ndiponso ali ndi manyazi aakulu. Makoma a Yerusalemu ngogamukagamuka, ndipo zipata zake zidaonongeka ndi moto.”

4Pamene ndidamva mau ameneŵa, ndidakhala pansi nkuyamba kulira, ndipo ndidalira masiku angapo. Ndinkasala chakudya, ndi kumapemphera kwa Mulungu wakumwamba.

5Ndidati, “Inu Chauta, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, mumasunga chipangano. Mumaonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu amene amakukondani ndi kutsata malamulo anu.

6Tsekulani maso ndipo tcherani khutu, kuti mumve pemphero la mtumiki wanune, limene ndikupereka tsopano kwa Inu usana ndi usiku, kupempherera Aisraele atumiki anu. Ndikuvomera machimo amene ife Aisraele tidakuchimwirani. Zoonadi, ine pamodzi ndi banja la makolo anga, tidakuchimwirani.

7Tidakuchitirani zoipa zambiri, ndipo sitidamvere mau anu, malamulo anu ndiponso malangizo amene mudapatsa Mose mtumiki wanu.

8Lev. 26.33 Kumbukirani mau amene mudauza Mose mtumiki wanu akuti, ‘Ngati mukhala osakhulupirika, ndidzakumwazani pakati pa anthu a mitundu ina.

9Deut. 30.1-5 Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuŵatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu omwazikawo akhale kutali chotani, ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku malo amene ndidasankha kuti azidzandipembedza kumeneko.’

10Iwoŵa ndiwo atumiki anu ndi anthu anu amene mudaŵapulumutsa ndi mphamvu yanu yaikulu ndi dzanja lanu lolimba.

11Inu Chauta, tcherani khutu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu ena amene amakonda kulemekeza dzina lanu. Lolani kuti ine mtumiki wanu zinthu zindiyendere bwino lero, ndipo kuti mfumu indichitire chifundo.”

Pa nthaŵi imeneyo nkuti ine ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help