2 Pet. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndine, Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa anthu amene adalandira chikhulupiriro chomwe ifenso tidalandirako. Iwonso adachilandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

2Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wochuluka, pakumdziŵa Iyeyo ndiponso Yesu Ambuye athu.

Mulungu adaitana ndi kusankha akhristu

3Mulungu mwa mphamvu zake adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa.

4Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa.

5Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo.

6Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko.

7Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.

8Ngati zonsezi zikhala mwa inu, nkumachuluka, simudzakhala olephera ndi opanda phindu pa nzeru zodziŵira Ambuye athu Yesu Khristu.

9Paja munthu wopanda zimenezi ndiye kuti ngwakhungu, sangathe kuwona patali, ndipo waiŵala kuti adamtsuka machimo ake akale.

10Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse.

11Choncho adzakutsekulirani kwathunthu khomo loloŵera mu Ufumu wosatha wa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu.

12Nchifukwa chake cholinga changa nchakuti ndizikukumbutsani zimenezi nthaŵi zonse, ngakhale mukuzidziŵa ndipo mumakhulupirira ndi mtima wonse choona chimene mudalandira.

13Ndiyesa nkoyenera kuti, ndikadali mu msasa uno, nditsitsimutse mitima yanu pakukukumbutsani zimenezi.

14Pakuti ndikudziŵa kuti nthaŵi yakutuluka mu msasa wanga uno yayandikira, monga andidziŵitsira Ambuye athu Yesu Khristu.

15Ndipo ndidzayesetsa kukonza zoti nditachoka ine, muzidzatha kuzikumbukira zimenezi nthaŵi iliyonse.

Mboni za ulumerero wa Khristu

16Ife sitidatsate nthano zongopeka chabe, pamene tidakudziŵitsani za mphamvu zao ndi za kubweranso kwao kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Koma tidachita kuuwona ndi maso athu ukulu wake.

17Mt. 17.1-5; Mk. 9.2-7; Lk. 9.28-35Iye adalandira ulemu ndi ulemerero kwa Mulungu Atate, ndipo adamufikira mau ochokera kwa Atate aulemererowo akuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.”

18Ndipo mau ameneŵa ifeifeyo tidaŵamva kuchokera kumwamba chifukwa tidaali naye pamodzi pa phiri loyera lija.

19Motero tikudziŵa ndithu tsopano kuti mau aja a anereriŵa ngoona. Nkwabwino tsono kuti muŵayang'anitsitse ngati nyale yoŵala m'malo amdima, kufikira nthaŵi imene kudzayambe kucha, pamene nyenyezi yam'mamaŵa idzayambe kuŵala m'mitima mwanu.

20Koma choyamba mumvetse kuti munthu payekha sangathe kumasulira mau a aneneri olembedwa m'Malembo.

21Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help