1Chauta, mtima wanga ndi wosadzikuza,
maso anga ndi osanyada.
Sinditengeka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
2Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga,
monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere.
Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
3Iwe Israele, khulupirira Chauta
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.