1 Eks. 12.1-20; Lev. 23.5-8; Num. 28.16-25 Muzilemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakuchita chikondwerero cha Paska pa mwezi wa Abibu. Chifukwa usiku wina mwezi umenewu, mpamene Chauta adakutulutsani ku Ejipito.
2Muzipereka nsembe za chikondwerero cha Paska kwa Chauta, Mulungu wanu. Muphe nkhosa kapena ng'ombe pa malo amene Chauta adzasankhule kuti anthu azidzapembedzerapo.
3Nyama ya nsembeyo musadye ndi buledi wotupitsa. Pa masiku asanu ndi aŵiri, muzidya nyamayo ndi buledi wosatupitsa ndiye kuti buledi wamazunzo, pakuti mudatuluka ku Ejipito mothaŵa. Motero masiku onse a moyo wanu, mudzakumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito.
4Pa masiku asanu ndi aŵiri munthu wina aliyense asadzasunge chofufumitsira buledi m'nyumba mwake m'dziko mwanumo. Nyama imene idaphedwa madzulo pa tsiku loyamba, muzidzaidya kusanache.
5Musapereke nsembe ya Paska kulikonse ku dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.
6Muziphera pa malo amodzi opembedzerapo aja. Muzichita zimenezi poloŵa dzuŵa, ndiye kuti nthaŵi yomwe ija imene mudachoka ku Ejipito.
7Muziphika nyamayo ndi kuidyera pa malo achipembedzo amodziwo, ndipo muzibwerera ku zithando zanu m'maŵa mwake.
8Masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wosatupitsa. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, muzisonkhana kuti mupembedze Chauta, Mulungu wanu, ndipo musadzagwire ntchito pa tsiku limenelo.
Za chikondwerero cha kholola(Eks. 34.22; Lev. 23.15-21)9 Lev. 23.15-21; Num. 28.26-31 Muŵerenge masabata asanu ndi aŵiri kuyambira nthaŵi imene mwayamba kudula tirigu.
10Tsono muchite chikondwerero cha kholola, cholemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakumpatsa chopereka chaufulu, molingana ndi madalitso amene Iye wakupatsani.
11Mukhale okondwa pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wamu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu pamodzi m'mizinda mwanu. Zimenezi muzichitira pa malo opembedzerapo aja.
12Kumbukirani kuti mudaali akapolo ku Ejipito. Motero malamulo ameneŵa muziŵasungadi mosamala.
Za chikondwerero cha misasa(Lev. 23.33-43)13 Lev. 23.33-36, 39-43; Num. 29.12-38 Mutatuta tirigu wanu yense, ndiponso mutafinya mphesa zanu, muzidzachita chikondwerero cha misasa masiku asanu ndi aŵiri.
14Musangalale pa chikondwererocho, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wanu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu m'mizinda mwanu.
15Muzidzatamanda Chauta, Mulungu wanu, pochita chikondwerero chimenechi masiku asanu ndi aŵiri, pa malo amene Iye adzasankhule, chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atadalitsa kholola lanu ndi ntchito zanu zonse, kuti chimwemwe chanu chikhale chodzaza ndithu.
16Anthu aamuna onse a mtundu wanu azidzabwera kudzapembedza Chauta, Mulungu wanu, ku malo achipembedzo, katatu pa chaka. Azidzafika pa nthaŵi ya Paska, pa nthaŵi ya chikondwerero cha kholola ndiponso pa nthaŵi ya chikondwerero cha misasa.
17Ndipo pobwera pamaso pa Chauta, asamadzakhale chimanjamanja, koma munthu aliyense azidzabwera ndi mphatso monga momwe angathere, molingana ndi madalitso amene Chauta, Mulungu wanu, adampatsa.
Za kuweruza kolungama18M'fuko lililonse mudzasankhe anthu oweruza ndiponso akuluakulu ena mu mzinda uliwonse umene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatseni. Anthu ameneŵa azidzaweruza anzao mosakondera.
19Eks. 23.6-8; Lev. 19.15 Asadzachite zinthu mopanda chilungamo kapena kuweruza milandu mokondera. Asadzalandire chiphuphu, chifukwa ziphuphu zimadetsa m'maso ngakhale anthu anzeru ndipo zimalakwitsa anthu olungama poweruza.
20Mukonde osati china ai, koma chilungamo chokha basi, kuti mudzalandiredi dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani ngati choloŵa chanu, ndi kukhazikikamo.
21 Eks. 34.13 Musadzazike mtengo uliwonse wachipembedzo pambali pa guwa la Chauta, Mulungu wanu, limene mudzamange.
22Lev. 26.1 Ndipo musadzaimiritse miyala yachipembedzo, popeza kuti Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo zimenezi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.