1Tsopano inu Aisraele, muzimvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukuphunzitsani, kuti mukhale ndi moyo. Ndipo mudzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani.
2Chiv. 22.18, 19 Musaonjezerepo kanthu kena pa zimene ndakulamulani, ndipo musachotsepo kanthu. Muzimvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatsani.
3Num. 25.1-9 Inu mudaona zimene Chauta adachita ku Baala-Peori. Kumeneko Chauta, Mulungu wanu, adaonongeratu onse amene ankapembedza Baala wa ku Peori,
4koma nonsenu amene mudakangamira Chauta, Mulungu wanu, muli ndi moyo lero lino.
5Ndakuphunzitsani malamulo ndi malangizo onse, monga momwe Chauta, Mulungu wanga, adandilamulira. M'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo, muzikamvera malamulo ameneŵa.
6Mukaŵasunge ndi kuŵatsata, ndipo chimenechi chidzaonetsa anthu a mitundu ina kuti ndinu anthu anzeru ndi omvetsa zinthu bwino. Akadzamva malamulo onseŵa, iwowo adzati, “Mtundu umenewu ndi waukulu, wanzeru ndi womvetsa zinthu bwino.”
7Palibe mtundu wina uliwonse, kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi Mulungu wokhala pafupi nawo, monga m'mene Mulungu wathu amakhalira ndi ife. Nthaŵi zonse tikamuitana, amatiyankha.
8Palibe mtundu wina uliwonse kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi malamulo ndi malangizo achilungamo onga aŵa amene ndakupatsani leroŵa.
9Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe.
10Muziŵauza za tsiku lija pamene mudaima pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, ku phiri la Horebu kuja. Kumeneko Chauta adandiwuza kuti, “Asonkhanitseni anthu. Ndifuna kuti iwo amve zimene ndilankhule, kuti aphunzire kundiwopa nthaŵi zonse adzakhale ndi moyo pa dziko lapansi, kenaka azidzaphunzitsanso ana ao kundimvera.”
11Eks. 19.16-18; Ahe. 12.18, 19 Inu mudadza, mudaima patsinde pa phiri. Phirilo linkayaka moto mokwera mpaka ku thambo, ndipo linali lophimbidwa ndi chiwutsi chabii ndi chimdima.
12Chauta adalankhula nanu ali m'motomo, ndipo munkamumva akulankhula, koma osamuwona.
13Eks. 31.18; 34.28; Deut. 9.10 Chauta adakuuzani zimene muyenera kuchita, kuti musunge chipangano chimene adapangana ndi inu, ndicho malamulo khumi amene adaŵalemba pa miyala iŵiri.
14Eks. 21.1 Chauta adandilamula nthaŵi imeneyo kuti ndikuphunzitseni malamulo amene muyenera kumaŵasunga m'dziko limene mukaloŵe ndi kukakhalamolo.
Aŵachenjeza kuti asapembedze mafano15Pamene Chauta adalankhula nanu ali m'moto pa phiri la Horebu lija, inu simudaone kanthu kalikonse. Nchifukwa chake muchenjere.
16Eks. 20.4; Lev. 26.1; Deut. 5.8; 27.15 Samalani kuti musachimwe pakudzipangira fano la mtundu uliwonse, kaya fanolo likhale longa mwamuna kaya mkazi,
17Aro. 1.23 fano la nyama iliyonse ya pa dziko lapansi, fano la mbalame iliyonse yamumlengalenga,
18fano la chilichonse chokwaŵa pa nthaka, ndi fano la nsomba iliyonse yam'madzi pansi pa dziko.
19Musamale kuti mukapenya ku thambo nkuwona dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi zonse zakuthamboko, mtima wanu usakopeke nkuyamba kupembedza ndi kutumikira zinthu zimene Mulungu wanu wapatsa anthu ena onse a pa dziko lapansi.
20Eks. 19.5; Deut. 7.6; 14.2; 26.18; Tit. 2.14; 1Pet. 2.9 Koma inu ndinu anthu amene Mulungu adakutulutsani ku dziko la Ejipito, ng'anjo yotentha ija. Adakutulutsanimo kuti mukhale anthu akeake monga m'mene muliri leromu.
21Num. 20.12 Chauta, Mulungu wathu, adandikwiyira ine chifukwa cha inu. Ndipo adalumbira kuti ine sindiwoloka mtsinje wa Yordani kukaloŵa m'dziko lokoma limene akukupatsanilo ngati choloŵa chanu.
22Ndidzafera m'dziko lomwe lino osaoloka mtsinjewo. Koma inu, muli pafupifupi kuwoloka ndi kukhala m'dziko lokomalo.
23Samalani bwino, musaiŵale chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, adachita nanu, ndipo musapange fano lofanizira chinthu chilichonse chimene Chauta, Mulungu wanu, adakuletsani.
24Ahe. 12.29 Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Ali ngati moto waukali.
25Ngakhale mutakhala m'dzikomo nthaŵi yaitali, ndi kubereka ana ndi zidzukulu, musadzachimwe pakudzipangira fano la maonekedwe ena aliwonse. Pamaso pa Chauta ndi zoipa zimenezi, ndipo adzapsa nazo mtima.
26Mukachita zimenezi, ndikukuuzani lero, kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni, kuti simudzakhalitsa pa dziko. Mudzaonongeka m'dziko ili la patsidya pa Yordani, limene mukukakhalamolo. Mudzaonongeka nonsenu.
27Deut. 28.36 Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu ina, ndipo oŵerengeka okha mwa inu ndiwo adzatsala pakati pa mitundu ina kumene Chauta adzakupirikitsirani.
28Kumeneko muzidzatumikira milungu yopanga ndi manja, monga yamtengo ndi yamwala, milungu imene singathe kupenya kapena kumva, kudya kapenanso kununkhiza.
29Yer. 29.13 Kumeneko inu mudzafunafuna Chauta, Mulungu wathu, ndipo ngati mudzamfunafuna ndi mtima wonse ndi moyo wanu wonse, mudzampeza.
30Mukadzakhala pa mavuto, ndipo zinthu zonsezi nkukuchitikirani, pamenepo mudzabwerera kwa Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzamvera mau ake.
31Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wachifundo. Sadzakulekererani kapena kukuwonongani. Chipangano chimene Iye adachita molumbira ndi makolo anu, sadzachiiŵala.
32Tafufuzani zakale, inu musanabadwe, kuyambira pa tsiku lija limene Mulungu adalenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani pa dziko lonse lapansi. Kodi chachikulu chonga chimenechi chidachitikapo ndi kale lonse? Kodi alipo wina amene adamvapo zotere?
33Kodi alipo anthu ena amene adakhalabe ndi moyo, atamva mau a Mulungu ali m'moto, monga m'mene mudamvera inu?
34Kodi alipo mulungu wina aliyense amene adaapita kukadzitengera anthu kuŵachotsa pakati pa fuko lina, naŵasandutsa anthu akeake, monga muja Chauta, Mulungu wanu, adakuchitirani inu ku Ejipito kuja? Iye adachita zimenezo ndi mphamvu zake zazikulu, inu mukupenya. Adadzetsa miliri pamodzi ndi nkhondo, adachita zozizwitsa ndi zodabwitsa.
35Mk. 12.32 Chauta adakuwonetsani zimenezi, kuti inu mudziŵe kuti Chauta yekha ndiye Mulungu, ndipo kuti palibenso wina.
36Chauta adalola kuti mumve mau ake kuchokera kumwamba, kuti pakutero akuphunzitseni. Pa dziko lapansi pano Chauta adakuwonetsani moto waukulu, ndipo mudamva akulankhula nanu kuchokera m'motomo.
37Popeza kuti Chauta adakonda makolo anu, adasankha inu zidzukulu zao nakutulutsani ku Ejipito pakuwonetsa ulemu ndi mphamvu zake zazikulu.
38Pamene munkayenda, Iye adapirikitsira kutali mitundu ikuluikulu kupambana inu, kuti akuloŵetseni ndi kukupatsani dziko laolo, kumene muli lero lino.
39Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai.
40Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani leroŵa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya.
Mizinda yopulumukiramo ya kuvuma kwa Yordani41 Yos. 20.8, 9 Pamenepo Mose adapatula mizinda itatu kuvuma kwa Yordani
42kumene munthu wopha mnzake mwangozi, osati mwachidani, ankatha kuthaŵirako ndi kupulumutsa moyo wake.
43A fuko la Rubeni, mzinda wao unali Bezeri umene unali m'chipululu, m'dziko lamapiri. A fuko la Gadi, mzinda wao unali Ramoti umene unali m'dziko la Giliyadi. Ndipo a fuko la Manase mzinda wao unali Golani umene unali m'dziko la Basani.
Mau oyamba popereka malamulo a Mulungu44Aŵa ndi malamulo amene Mose adapatsa Aisraele.
45Ameneŵa ndi malamulo ndi mau ndiponso malangizo amene Mose adauza Aisraele, atatuluka ku Ejipito.
46Aisraelewo anali m'chigwa kuvuma kwa mtsinje wa Yordani, kuyang'anana ndi mudzi wa Betepeori. Kumeneko ndi dziko la Sihoni, mfumu ya Aamori, amene ankalamula mzinda wa Hesiboni, ndipo Mose ndi Aisraelewo atatuluka m'dziko la Ejipito, adamgonjetsa Sihoniyo.
47Aisraele aja adakakhala m'dziko lake ndi m'dziko la mfumu Ogi wa ku Basani. Ameneŵa anali mafumu aŵiri a Aamori amene ankakhala kuvuma kwa Yordani.
48Dziko limene adalandalo lidayambira ku mudzi wa Aroere pamphepete pa mtsinje wa Arinoni, mpaka kukafika ku phiri la Sirioni (ndiye kuti phiri la Heremoni),
49ndi dziko lonse la Araba la kuvuma kwa mtsinje wa Yordani, mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, patsinde pa phiri la Pisiga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.