1Tamandani Chauta!
Tamandani Chauta inu okhala kumwamba,
mtamandeni inu okhala mu mlengalenga!
2Mtamandeni inu angelo ake onse,
mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse!
3Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi,
mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala!
4Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba,
ndi inu madzi a pamwamba pa thambo!
5Zonsezo zitamande dzina la Chauta!
Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa.
6Adazikhazikitsa kuti zikhale mpaka muyaya,
adaikapo lamulo limene silingathe kusinthika.
7Tamandani Chauta inu okhala pa dziko lapansi,
inu zilombo za m'madzi ndi nyanja zonse zozama,
8inu moto ndi matalala, inu chisanu chambee ndi mitambo,
inu mphepo zamkuntho, okwaniritsa zolamula Chauta!
9Inu mapiri onse ndi zitunda zonse,
inu mitengo yazipatso ndi mikungudza yonse!
10Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse,
inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka!
11Inu mafumu a pa dziko lapansi
ndi anthu a mitundu yonse,
inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi!
12Inu anyamata pamodzi ndi anamwali,
inu nkhalamba ndi ana omwe!
13Onsewo atamande dzina la Chauta,
pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka,
ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe.
14Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu.
Walemekeza anthu ake onse oyera mtima,
Aisraele amene Iye amaŵakonda.
Tamandani Chauta!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.