Yer. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aneneratu za Mesiya Mfumu yam'tsogolo

1“Tsoka kwa abusa amene amaononga ndi kumwaza nkhosa za pabusa panga,” akutero Chauta.

2Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wa Israele, ponena za abusa oyang'anira anthu ake, akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga, simudazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu.

3Pambuyo pake Mwiniwakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku malo onse amene ndidazimwazira. Ndidzazibwezera ku busa lakwao, ndipo zidzaswana ndi kuchuluka.

4Ndidzazipatsa abusa oziŵeta bwino. Sizidzaopanso kapena kuchita mantha, kapena kusokera,” akuterotu Chauta.

5 Yer. 33.14-16 Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzaphukitsira Davide nthambi yoongoka imene idzakhala mfumu yanzeru ndi yoweruza m'dzikomo mwachilungamo ndi mosakondera.

6Pa masiku akewo Yuda adzapulumuka, ndipo Israele adzakhala pabwino. Adzamutcha dzina ili lakuti, ‘Chauta ndiye chilungamo chathu.’ ”

7Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene anthu polumbira sazidzatinso, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko la Ejipito!’

8Koma azidzati, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku maiko konse kumene adaŵabalalitsira.’ Ndithu ndidzaŵabwezera ku malo amene ndidapatsa makolo awo.”

Za aneneri onama

9Kunena za aneneri, mtima wanga wasweka,

m'nkhongono mwachita kuti zii!

Ndakhala ngati munthu woledzera,

munthu wosokonezeka ndi vinyo,

chifukwa cha Chauta ndi mau ake oyera.

10Dziko lino ladzaza ndi anthu achigololo.

Chifukwa cha temberero la Chauta m'dziko

mwagwa chilala,

mabusa akuchipululu auma.

Amene amangothamangira zoipa,

amalimbikira kuchita zosalungama.

11“Zoonadi, aneneri ndiponso ansembe,

onsewo saopa Mulungu.

Ndaŵapeza akuchita zoipa ngakhale m'Nyumba mwanga,”

akutero Chauta.

12“Nchifukwa chake njira zao zidzakhala zoterera.

Adzaŵapirikitsira kumdima kumene akagwe.

Ndidzaŵaonetsa ndoza pa nthaŵi ya chilango chao,”

akuterotu Chauta.

13“Pakati pa Aneneri a ku Samariya

ndaonapo choipa ichi:

ankalosa m'dzina la Baala,

motero adasokeza anthu anga Aisraele.

14 Gen. 18.20; Ezek. 16.49 Pakati pa aneneri a ku Yerusalemunso

ndaonapo chinthu choopsa kwambiri:

amachita zigololo, amanena bodza,

ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoipa,

kotero kuti palibe amene amaleka machimo ake.

Kwa Ine onsewo ali ngati anthu a ku Sodomu ndi Gomora.”

15Chifukwa cha zimenezi,

ponena za aneneri ameneŵa,

Chauta akuti,

“Ndidzaŵadyetsa dzoŵaŵa

ndi kuŵamwetsa madzi azumu,

chifukwa zoipa zimene zaŵanda m'dziko lonse

zachokera kwa aneneri omweŵa.”

16Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai.

17Saleka kuŵauza amene amandinyoza Ine kuti, ‘Zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Ndipo amene amaumirira kutsata zofuna za mtima wao amaŵauza kuti, ‘Simudzaona vuto ai.’ ”

18Ine ndidati,

“Mwa aneneriwo ndani amene adakhala

nao m'bungwe la Chauta?

Ndani adamuwona ndi kumva mau ake?

Ndani mwa iwo adasamalako mau ake ndi kuŵamvera?

19Onani mphepo yamkuntho yochokera kwa Chauta!

Onani ukali wake woomba ngati namondwe,

udzaomba pa mitu ya anthu oipa.

20Mkwiyo wa Chauta sudzaleka,

mpaka atachita zonse zimene adatsimikiza

mumtima mwake.

Zimenezi mudzazidziŵa masiku akubweraŵa.”

21Chauta adati,

“Aneneri ameneŵa sindidaŵatume ndine,

komabe ankathamanga uku ndi uku ndi mithenga yao.

Sindidalankhule nawo,

komabe ankalosa.

22Akadakhala nane pa bungwe langa,

bwenzi atalalikadi mau anga kwa anthu anga.

Bwenzi ataŵachotsa m'njira zao zoipa,

kuti aleke machimo ao.”

23Chauta akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi, koma ndikakhala patali ndiye kuti sindinenso Mulungu?

24Lun. 1.7; Mphu. 16.17Kodi munthu nkubisala pobisika potani, pamene Ine sindingathe kumuwona? Kodi Ine sindili ponseponse, kumwamba ndi pa dziko lapansi pano?” Akuterotu Chauta.

25“Ndamva zimene aneneri akulankhula, aneneri amene akulosa zabodza m'dzina langa, nkumafuula kuti, ‘Ndalota, ndalota.’

26Kodi zabodzazi adzazisunga mumtima mwao mpaka liti aneneri onamaŵa, amene amalosa zonyenga za mumtima mwao?

27Aneneri ameneŵa amakhulupirira kuti anthu anga adzandiiŵala akamamva zamalotozo, monga momwe makolo ao adaiŵalira dzina langa pomapembedza Baala.

28Ngati mneneri walota maloto, afotokoze maloto akewo. Koma amene ali ndi mau anga, alalike mau angawo moona. Kodi mungu ungafanane ndi tirigu?” Akuterotu Chauta.

29“Kodi suja mau anga amatentha ngati moto? Kodi suja mau anga ali ngati nyundo imene imaphwanya thanthwe?

30“Nchifukwa chake ndikuŵakana aneneri amene amaberana mau iwo okhaokha nkumati mauwo ndi a Ineyo.

31Ndikuŵatsutsa aneneri amene amakonda kulankhula zamabodza, namanena kuti, ‘Ameneŵa ndiwo mau a Chauta.’

32Ndikuŵakana aneneri amene amalota zabodza, namasimbira anthu anga ndi kumaŵasokeza ndi mabodza aowo. Sindidaŵatume ndine kapena kuŵalamula, ndipo sathandiza anthu mpang'ono pomwe,” akuterotu Chauta.

Za katundu wolemera wa Chauta

33Chauta adauza Yeremiya kuti, “Anthu ameneŵa, kaya ndi mneneri, kaya ndi wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Chauta ukuti chiyani?’ Udzayankhe kuti, ‘Inuyo ndiye katundu wolemetsa Chauta, ndipo adzakutayani,’ akuterotu Chauta.

34Ndipo mneneri, wansembe, kapena munthu wina aliyense, wonena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta,’ ameneyo ndidzamulanga pamodzi ndi banja lake.

35Koma mau amene aliyense azifunsa mnzake kapena mbale wake akhale akuti, ‘Kodi Chauta wanena zotani?’

36Koma musanenanso kuti ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta.’ Uthenga wa aliyense ndi mau a iye mwini, motero inuyo mudapotoza mau a Mulungu wamoyo, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.

37Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Chauta wayankha zotani?’ Kapena kuti, ‘Kodi Chauta wanena zotani?’

38Koma ngati munena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta,’ Chautayo akuti, ‘Popeza kuti mwanena mau akuti nawu uthenga wolemetsa wa Chauta, pamene ndidakuuzani kuti musanene mau ameneŵa,

39pamenepo Ine mwini ndidzakunyamulani ngati katundu wolemetsa nkukutayani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndidakupatsani inu ndi makolo anu.

40Ndidzakunyozani mpaka muyaya, ndikakuchititsani manyazi osaiŵalika.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help