Ahe. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za Yesu Mkulu wa ansembe wathu

1 Mas. 110.1 Mfundo yeniyeni pa zimene tikunenazi ndi iyi: tili naye wotere Mkulu wa ansembe onse, amene akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu Waulemerero Kumwamba.

2Iye akutumikira m'Malo Opatulika am'katikati, ndiye kuti m'chihema chenicheni chimene adachimanga ndi Ambuye osati munthu ai.

3Paja mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu. Motero nkofunika kuti wathunso mkulu wa ansembe onse akhale nkanthu koti apereke.

4Iyeyu akadakhala pa dziko lapansi, sibwenzi ali wansembe konse, popeza kuti alipo kale ansembe amene amapereka mphatso potsata Malamulo a Mose.

5Eks. 25.40 Ntchito za chipembedzo zimene iwo amachita, zili ngati chithunzi chongofanizira zenizeni za Kumwamba. Paja zidaateronso ndi Mose: pamene iye adaati amange chihema, Mulungu adaamlangiza kuti, “Upangetu zonse molingana ndi chitsanzo chimene ndidaakuwonetsa paphiri paja.”

6Koma monga zilirimu, Yesu adalandira unsembe wopambana kutalitali unsembe wakale uja, monga momwe ndiyenso Nkhoswe ya chipangano chopambana, chifukwa malonjezo ake ngopambana malonjezo a chipangano chakale chija.

7Chipangano choyamba chija chikadakhala changwiro, sipakadafunikanso china m'malo mwake.

8Yer. 31.31-34 Koma Mulungu adadzudzula anthu ake ndi mau aŵa akuti,

“Masiku akubwera,

pamene ndidzachita chipangano chatsopano

ndi fuko la Israele,

ndiponso ndi fuko la Yuda.

9Sichidzakhala chonga chipangano

chimene ndidaachita ndi makolo ao

tsiku limene ndidaachita kuŵagwira pa dzanja

kuti ndiŵatulutse m'dziko la Ejipito.

Chifukwa iwo sadasunge chipangano changa chija,

nanenso sindidaŵasamale”,

akutero Ambuye.

10“Nachi tsono chipangano

chimene ndidzachita ndi fuko la Israele

atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye:

“Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao

ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao.

Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao,

iwowo adzakhala anthu anga.

11Sipadzafunikanso kuti wina aliyense aphunzitse mnzake,

kapena kuti wina aliyense auze mbale wake kuti,

‘Udziŵe Ambuye’.

Pakuti onse adzandidziŵa,

kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu.

12Mwachifundo ndidzaŵakhululukira zochimwa zao,

sindidzakumbukiranso machimo ao.”

13Pakunena mau oti, “Chipangano chatsopano”. Mulungu akunena kuti chipangano choyamba nchotha ntchito. Paja chinthu chimene chayamba kutha ntchito nkumakalamba, ndiye kuti chili pafupi kuzimirira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help