Ntc. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mzimu Woyera abwera

1 Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuŵamva anthuŵa akulankhula m'zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”

12Onse adazizwa ndi kuthedwa nzeru, ndipo adayamba kufunsana kuti, “Kodi chimenechi nchiyani?”

13Koma ena ankangoseka nkumati, “Aledzera vinyo watsopano.”

Petro aphunzitsa anthu

14Koma Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga.

15Anthuŵa sadaledzere ai, monga mukuganizira inu, pakuti nthaŵi idakali 9 koloko m'maŵa.

16Koma zimenezi ndi zomwe mneneri Yowele adalosa kuti,

17 .

43Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita.

44Ntc. 4.32-35Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao.

45Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.

46Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu.

47Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help