Mas. 57 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizoKwa Woimbitsa Nyimbo. Kutsata maimbidwe a nyimbo yoti: Musaononge. Salmo la Davide la mtundu wa Mikitamu. Anali atathaŵa kwa Saulo, kukaloŵa m'phanga.

1Mundichitire chifundo Inu Mulungu,

mundichitire chifundo,

pakuti mtima wanga ukudalira Inu.

Ndidzathaŵira pansi pa mapiko anu,

mpaka chiwonongeko chitandipitirira.

2Ndikulirira Mulungu Wopambanazonse,

Mulungu amene amandichitiradi zonse zimene walonjeza.

3Mulungu adzandiyankha ali kumwamba,

ndipo adzandipulumutsa.

Iye adzasokoneza amene andipondereza.

Adzaonetsa chikondi chake chosasinthika,

adzaonetsa kukhulupirika kwake.

4Ndimagona pakati pa anthu olusa

amene ali ngati mikango.

Mano ao ali ngati mikondo ndi mivi,

lilime lao lili ngati lupanga lakuthwa.

5Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu kumwambamwamba,

wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi.

6Iwo aja adatchera mapazi anga ukonde.

Mtima wanga umavutika kwambiri.

Akumba mbuna m'njira yanga,

koma agweramo okha.

7Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka,

ndithu mtima wanga wakonzekadi.

Ndidzaimba nyimbo,

nyimbo yake yotamanda.

8Lumpha iwe mtima wanga.

Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani,

Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga.

9Ndidzakuthokozani, Inu Chauta,

pakati pa mitundu ya anthu.

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani

pakati pa anthu a maiko onse,

10pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu,

chofika mpaka mlengalenga,

kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.

11Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu mumlengalenga monse.

Wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help