1Mose, munthu wa Mulungu uja, asanafe, adapereka madalitso kwa Aisraele.
2Poŵadalitsapo adanena mau akuti,
“Chauta adabwera kuchokera ku phiri la Sinai,
natitulukira kuchokera ku Seiri,
ndipo adatiŵalira kuchokera ku phiri la Parani.
Angelo zikwi khumi anali naye pamodzi,
moto woyaka unali m'manja mwake.
3Chauta amakonda anthu ake
ndipo amatchinjiriza onse
amene ali opatulikira Iye.
Anthuwo amaphunzira kwa Chauta,
amamvera malangizo ake,
4ndiye kuti malamulo amene adatipatsa Mose.
Malamulowo ndi chuma chopambana cha mtundu wa Yakobe.
5Chauta adakhala mfumu ya anthu ake Aisraele,
pamene mafuko ao ndi atsogoleri ao
adasonkhanitsidwa pamodzi.”
6Ponena za fuko la Rubeni, Mose adati,
“Rubeni asafafanizike, akhalitse ndithu,
ngakhale anthu ake ali pang'ono.”
7Za fuko la Yuda, adati,
“Inu Chauta, mverani pamene iwo akulira,
athandizeni, ndipo muŵalumikizenso ndi mafuko ena.
Inu Chauta, muŵalimbikitse kuti adziteteze okha,
ndipo muŵathandize polimbana ndi adani ao.”
8 Eks. 28.30; Eks. 17.7; Eks. 17.7; Num. 20.13 Za fuko la Levi adati,
“Inu Chauta, Tumimu ndi Urimu adziŵitse kufuna kwanu
kudzera mwa Alevi, atumiki anu okhulupirika.
Mudaŵayesa ku Masa kuja,
ndipo mudalimbana nawo ku madzi a Meriba kuja.
9Iwo adaonetsa kuti ankakhulupirira Inu
kupambana makolo ao, abale ao kapenanso ana ao.
Adamvera malamulo anu,
ndipo adakhulupirika pa chipangano chanu.
10Iwowo ndiwo adzaphunzitse ana a Yakobe
malangizo anu ndi Aisraele malamulo anu.
Adzafukiza lubani pamaso panu,
adzapereka nsembe zathunthu zopsereza pa guwa lanu.
11Inu Chauta, thandizani fuko lao
kuti likhale lamphamvu,
zochita zao zikukondwetseni.
Otsutsana nawo ndi odana nawo onse muŵaononge,
kotero kuti asadzadzukenso.”
12Za fuko la Benjamini adati,
“Fuko ili ndilo limene Chauta amalikonda,
ndipo amalitchinjiriza.
Tsiku ndi tsiku Chauta amalisunga,
pokhala m'kati mwa dziko laolo.”
13Za fuko la Yosefe adati,
“Chauta adalitse dziko lao,
likhale la mvula yambiri,
ndipo la zitsime zochuluka.
14Dziko lao lidalitsidwe
pokhala ndi zipatso zopsa ndi dzuŵa,
likhalenso ndi zokolola zochuluka pa nyengo iliyonse.
15Mapiri ao akalekaleŵa akutidwe ndi zipatso,
ndipo adzazidwe ndi zokolola zochuluka.
16Dziko lao likhale ndi dzinthu dzopambana,
lidalitsidwe ndi zokoma za Chauta
amene adalankhula m'chitsamba choyaka chija.
Madalitso onseŵa atsikire fuko la Yosefe,
popeza kuti anali mtsogoleri pakati pa abale ake.
17Yosefe ali ndi mphamvu zonga za ng'ombe yamphongo,
nyanga zake ndi zonga za njati,
adzapirikitsa anthu a mitundu ina ndi nyanga zimenezi.
Onsewo adzaŵapirikitsira ku malekezero a dziko.
Nyanga zimenezi ndi anthu zikwi khumi za Efuremu
ndipo anthu zikwi za Manase.”
18Za mafuko a Zebuloni ndi Isakara, adati,
“Zebuloni akondwere pa malonda ake,
Isakara akondwere m'zithando mwake.
19Ku mapiri ao amaitanirako mitundu ya anthu,
kumeneko amaperekako nsembe zoyenera,
chifukwa choti amapeza chuma pochita malonda m'nyanja,
kuchokera mu mchenga wa m'mbali mwa nyanja.”
20Za fuko la Gadi, adati,
“Alemekezeke Chauta amene adakulitsa dziko la Gadi.
Gadi amalalira ngati mkango waukazi,
amamwetula dzanja ndi bade la mutu lomwe.
21Adadzitengera dziko labwino kuti likhale lao,
gawo la mtsogoleri lidaperekedwa kwa iwowo.
Adasunga maweruzo ndi malamulo a Chauta
pamene atsogoleri a Aisraele adasonkhanitsidwa pamodzi.”
22Za fuko la Dani adati,
“Dani ali ngati mwana wamkango,
amene amalumpha kuchokera ku Basani.”
23Za fuko la Nafutali, adati,
“Chauta wakomera mtima Nafutali namdalitsa kwambiri.
Dziko lake lifika mpaka kumwera
kuchokera ku nyanja ya Galileya.”
24Za fuko la Asere, adati,
“Asere ndi wodalitsidwa kupambana mafuko ena.
Abale ake amkonde,
dziko lake likhale lachuma, la mitengo ya olivi.
25Midzi yake itchinjirizidwe
ndi zitseko zachitsulo m'malinga,
mphamvu zake zikhalitse monga masiku a moyo wake.”
26Inu Aisraele, palibe mulungu wina
wofanafana ndi Mulungu wanu,
amene amayenda ndi ulemerero mu mlengalenga,
amakwera pa mitambo namabwera kudzakuthandizani.
27Chauta ndiye amene ali kothaŵirako
ndipo pa dziko lapansili amakusungani
ndi mphamvu zosatha.
Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda,
ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
28Motero Aisraele ali pa mtendere,
zidzukulu za Yakobe zikusungidwa bwino m'dzikomo
m'mene tirigu ndi vinyo sizisoŵa,
m'mene mame amangogwa kuchokera kumwamba.
29Iwe Israele, ndiwetu wodala,
wofanafana nawe palibe.
Ndiwe mtundu umene Chauta adaupulumutsa.
Chauta weniweniyo ndiye chishango chako ndi lupanga lako,
ndiye amene amakutchinjiriza ndi kukupambanitsa.
Adani ako adzafika kudzapempha kuti uŵachitire chifundo,
koma iwe udzaŵapondereza pansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.