1 2Maf. 25.1-7 Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa chaka cha khumi cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, chimene chinali chaka cha 18 cha ufumu wa Nebukadinezara.
2Pa nthaŵi imeneyo ankhondo a mfumu ya ku Babiloni ankazinga Yerusalemu ndi zithando zankhondo. Mneneri Yeremiya anali atamtsekera m'bwalo la alonda, m'kati mwa nyumba yaufumu ya ku Yuda.
3Zedekiya mfumu ya ku Yuda ndiye amene adaamtsekera m'menemo. Mfumuyo idaamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani iwe ukulosa zakuti, Chauta akunena kuti, ‘Mzindawu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.
4Zedekiya mfumu ya ku Yuda sadzapulumuka kwa Ababiloni, koma adzaperekedwa ndithu kwa mfumu ya ku Babiloni. Adzaonana naye maso ndi maso nadzalankhula naye.
5Zedekiya adzatengedwa kupita ku Babiloni, ndipo adzakhala kumeneko mpaka nditamkhaulitsa, akutero Chauta. Ngakhale iye adzamenyane nawo chotani Ababiloniwo, sadzatha kuŵapambana.’ ”
6Yeremiya adanena kuti, “Chauta adandiwuza kuti
7Hanamele, mwana wa Asalumu, amalume anga, akudzandiwona, ndipo adzandiwuza kuti, ‘Gula munda wanga wa ku Anatoti, poti iweyo ndiye woyenera kuuwombola.’
8Monga momwe Chauta adanenera, Hanamele msuweni wanga adadzandiwonadi ku bwalo la alonda. Iyeyo adati, ‘Gula munda wanga ku Anatoti m'dziko la Benjamini, poti iwe ndiye woyenera kuuwombola kuti ukhale choloŵa chako.’ Tsono ndidadziŵa kuti umenewu unali uthenga wa Chauta uja.
9Motero ndidagula mundawo ku Anatoti kwa Hanamele msuweni wanga, ndipo mtengo wake unali masekeli asiliva 17.
10Ndidasaina chipanganocho ndi kuchimata pamaso pa mboni, kenaka nkuyesa ndalamazo pa sikelo.
11Pambuyo pake ndidatenga makalata anga a chipangano, ina yomata, m'mene munali mau onse a chipangano, ndi ina yosamata.
12Makalatawo ndidaŵapereka kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya, pamaso pa Hanamele msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zidaasaina chipanganocho, ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la alonda.
13Ndidamlangiza Baruki pamaso pa onsewo kuti,
14Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, walamula kuti iweyo utenge makalata a umboni wa chipanganoŵa, inai yomata inai yosamata, uŵasunge m'mbiya kuti akhale nthaŵi yaitali.
15Ndithudi Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akutitu idzafika nthaŵi pamene anthu azidzagulanso nyumba, minda ndi mitengo ya mphesa m'dziko lino.”
Pemphero la Yeremiya16Nditampatsa Baruki, mwana wa Neriya, makalata a chipangano aja, ndidayamba kupemphera kwa Chauta, ndidati,
17“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
18Mumaonetsa chikondi chanu chosasinthika kwa anthu osaŵerengeka. Ndipo mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo ao. Inu Mulungu wamkulu ndi wamphamvu, dzina lanu ndinu Chauta Wamphamvuzonse.
19Zolinga zanu nzazikulu, ndipo ntchito zanu nzamphamvu. Maso anu amaona makhalidwe onse a anthu. Ndipo aliyense mumampatsa mphotho malinga ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake.
20Inu mudachita zizindikiro zozizwitsa ndi ntchito zododometsa ku Ejipito, ndipo mwakhala mukuzichitabe mpaka pano, pakati pa Israele ndiponso pakati pa anthu onse. Motero mwatchukitsa dzina lanu mpaka lero lino.
21Inu ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri mudatulutsadi anthu anu Aisraele ku Ejipito pochita zizindikiro zozizwitsa ndi ntchito zododometsa zimene zidaopsa adani athu.
22Mudaŵapatsa dziko lino, limene mudalonjeza makolo ao molumbira, dziko lamwanaalirenji.
23Adaloŵa nkulilanda kuti likhale lao. Koma iwo sadakumvereni, sadatsate malamulo anu. Sankachita zimene mudaaŵalamula. Nchifukwa chake mwaŵagwetsera mavuto onseŵa.
24Onani, adani akuzinga ndi nthumbira zankhondo mzindawu kuti aulande. Mzinda umenewu udzaperekedwa kwa Ababiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Zimene munkanena zija zachitikadi, monga mwadziwonera nokha.
25Komabe ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababiloni, Inu Chauta mudandilamula kuti ndigule mundawo pali mboni ziŵiri.”
26Chauta adauza Yeremiya kuti,
27“Ine ndine Chauta, Mulungu wa anthu onse. Kodi chilipo choti Ine nkundikanika?
282Maf. 25.1-11; 2Mbi. 36.17-21 Nchifukwa chake Ineyo ndikunena kuti ndidzapereka mzindawu kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Iyeyo adzaulanda,
29ndipo Ababiloni amene akuuthira nkhondo, adzaloŵamo. Adzautentha ndi kugwetsa makamaka nyumba zimene padenga pake anthu ankandipsetsa mtima pofukizapo lubani kwa Baala ndi poperekapo chopereka cha chakumwa kwa milungu ina.
30Chiyambire pa ubwana wao, Aisraele ndi Ayuda akhala akungochita zoipa pamaso panga, nkumandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa,” akutero Chauta.
31“Mzinda umenewu wakhala ukuutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira nthaŵi imene adaumanga mpaka lero lino. Nchifukwa chake ndiyenera kuuchotsa pamaso panga.
32Aisraele ndi Ayuda, mafumu ao, akalonga, ansembe, aneneri, pamodzi ndi onse okhala ku Yerusalemu ndi ku Yuda, adandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa.
33Andifulatira kotheratu. Ngakhale ndidavutikira kumaŵaphunzitsa, sadamve kapena kutolapo nzeru iliyonse.
342Maf. 23.10; Yer. 7.30, 31; 19.1-6 Adaika mafano ao onyansa m'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo adaiipitsa.
352Maf. 23.10; Yer. 7.31; Lev. 18.21 Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala m'chigwa cha Benihinomu, kuti apereke ana ao aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Sindidalamule zimenezo ndine, ndipo sindidaganizeko kuti iwo nkuchita zonyansa zoterezi, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda pakutero.”
Za madalitso akutsogolo36Anthu ponena za mzinda umenewu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Komatu zimene Chauta, Mulungu wa Israele akunena ndi izi:
37Akuti, “Ine ndidzaŵasonkhanitsa anthuŵa kuchokera ku maiko onse kumene ndidaŵapirikitsira ndili wokwiya, waukali ndi wopsa mtima kwambiri. Ndidzaŵabwezanso ku malo ano, ndipo adzakhala kuno ndi mtendere wonse.
38Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.
39Ndidzaŵapatsa mtima umodzi ndi mkhalidwe umodzi, kotero kuti azidzandiwopa nthaŵi zonse. Motero iwowo ndi ana ao omwe, zinthu zidzaŵayendera bwino.
40Ndidzachita nawo chipangano chosatha. Sindidzaleka kuŵachitira zabwino. Ndidzaŵapatsa mtima wondiwopa, motero sadzandisiyanso.
41Ndidzakondwera kuŵachitira zabwino. Ndipo ndidzaŵakhazikitsa m'dziko lino mokhulupirika ndi mtima wanga wonse ndi kufuna kwanga konse.”
42Chauta akunena kuti, “Monga momwe ndidaŵaonongera anthuŵa, momwemonso ndidzaŵapatsa mtendere umene ndidzaŵalonjeza.
43Anthu adzagulanso minda m'dziko lino limene inu mumati nlosiyidwa, lopanda munthu ndi nyama yomwe, chifukwa adalipereka kwa Ababiloni.
44Anthu adzaguladi minda ndi ndalama. Mapangano ake adzalembedwa, adzamatidwa ndipo padzakhala umboni wake ku dera la Benjamini, ku malo oyandikana ndi Yerusalemu, m'mizinda ya ku Yuda, m'mizinda yakumapiri, m'mizinda yakuchigwa ndi yakumwera ku Negebu. Zoona, ndidzaŵabwezera ufulu wao,” akuterotu Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.