1 Bar. 4.12 Ha! Mzinda wa Yerusalemu wakhala wokhawokha,
m'menemo kale udaali wodzaza ndi anthu!
Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu,
koma tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye.
Kale unali mzinda wolemekezeka koposa mizinda ina,
koma tsopano wasanduka kapolo.
2Ukungolira usiku wonse,
misozi ikungoti mbwembwembwe pamasaya pake.
Mwa onse amene ankaukonda,
palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala
woti aziwusangalatsa.
Abwenzi ake onse auchita zaupandu,
onse asanduka adani ake.
3Ayuda apita ku ukapolo kukazunzika,
ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga.
Akukhala m'maiko ena,
osaona malo opumulira.
Onse oŵapirikitsa aŵapeza,
ali pa mavuto zedi.
4Miseu yopita ku Ziyoni yaŵirira,
chifukwa palibe wopitako
kuti akapembedze pa masiku achikondwerero.
Zipata zake zonse zili pululu,
ansembe ake akungodandaula.
Anamwali ake aja mtima wao ukupweteka,
ndithu Ziyoni ali pa masautso oopsa.
5Adani ake asanduka omulamulira,
odana naye akupeza bwino,
popeza kuti Chauta wamugwetsa m'mavuto
chifukwa cha machimo ochuluka a anthu ake.
Ana ake amuchokera,
atengedwa ukapolo ndi adani.
6Ulemerero wonse wa Ziyoni wachokeratu.
Akalonga ake asanduka ngati mphoyo zosoŵa msipu.
Ankathaŵa opanda ndi mphamvu zomwe, pofika adani.
7Pa masiku a mavuto ake ndi a kuzunzika kwake,
Yerusalemu amakumbukira zabwino zonse
zimene anali nazo masiku amakedzana.
Pamene anthu ake adagwa m'manja mwa adani,
panalibe womuthandiza.
Adani ake ankamupenyetsetsa monyodola
namaseka kugwa kwake.
8Yerusalemu adachimwa kwambiri,
motero wasanduka wonyansa.
Onse amene ankamulemekeza, akumunyoza tsopano,
chifukwa aona maliseche ake.
Iyeyo akungobuula ndipo akuyang'ana kumbali.
9Uve wake unkaonekera poyera,
iye osaganizako za tsoka lake lakutsogolo.
Nchifukwa chake kugwa kwake kunali koopsa,
ndipo panalibe womuthuzitsa mtima.
Akungoti,
“Inu Chauta, muyang'ane mavuto anga,
pakuti adani anga apambana.”
10Adani adamulanda chuma chake chonse.
M'malo ake oyera mudaloŵa anthu a mitundu ina,
amene Inu Chauta mudaŵaletsa kuloŵa mumsonkhano mwanu.
11Anthu ake onse amabuula akamafunafuna chakudya.
Chuma chao amagulitsana ndi chakudya,
kuti apezenso mphamvu.
Akuti, “Inu Chauta penyani,
muwone m'mene akundinyozera.”
12Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe,
inu amene mukudutsanu?
Tangopenyani, muwone
ngati pali mavuto ena onga angaŵa,
mavuto amene Chauta adandigwetsamo,
pamene adandikwiyira koopsa.
13Adatumiza moto kuchokera Kumwamba.
Udaloŵa mpaka m'kati mwa mafupa anga.
Adayala ukonde kuti akole mapazi anga, nandibweza.
Adandisiya ndili ndi chisoni chachikulu,
ndili wolefuka tsiku lonse.
14Zolakwa zanga adazimanga pamodzi
kuti zikhale ngati goli.
Adazimanga ndi manja ake.
Adazimangirira m'khosi mwanga,
adafooketsa mphamvu zanga.
Chauta wandipereka kwa anthu
amene sindingathe kulimbana nawo.
15Chauta adaŵamwaza anthu anga onse amphamvu
amene ankakhala nane.
Adasonkhanitsa gulu lina la anthu
kuti liwononge anyamata anga.
Chauta adapondereza Ayuda, anthu ake opatulika,
monga m'mene anthu amachitira mphesa mopondera mwake.
16Chifukwa cha zimenezi ndikulira,
misozi ili mbwembwembwe m'masomu.
Pakuti wondisangalatsa sali pafupi,
wondilimbitsa mtima ali kutali.
Anthu anga asiyidwa chifukwa mdani watigonjetsa.
17Ziyoni wakweza manja,
koma palibe ndi mmodzi yemwe womusangalatsa.
Chauta adalamula
kuti Yakobe anansi ake asanduke adani ake.
Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao.
18Pamenepo Chauta wakhoza,
chifukwa ndine ndidapandukira malamulo ake.
Imvani, inu anthu a mitundu yonse,
onani kuvutika kwanga.
Anamwali anga ndi anyamata anga atengedwa ukapolo.
19Ndidaitana abwenzi anga,
koma iwo adanditaya.
Ansembe anga ndi akuluakulu anga adafa mu mzinda,
pamene ankafunafuna chakudya
kuti mphamvu zao zibwereremo,
20Onani Inu Chauta m'mene ndavutikira mumtima mwanga,
moyo wanga wazunzika zedi.
Mtima wanga wakongonyala,
chifukwa choti ndapanduka kwambiri.
Mu mseu anthu akuphedwa ndi lupanga,
m'nyumbanso ndi imfa yokhayokha.
21Anthu akundimva pamene ndikudandaula,
koma palibe wondisangalatsa.
Adani anga onse atamva za tsoka langa,
adakondwa chifukwa cha zimene mudachita.
Tsiku limene mudalonjeza lija mulifikitse ndithu.
Nawonso adzasauke ngati ine ndemwe.
22Ntchito zao zonse zoipa mudzaŵaimbe nazo mlandu.
Muŵalange monga mudandilangira ine
chifukwa cha zolakwa zanga zonse.
Ndikubuula kwambiri,
ndipo mtima wanga wafookeratu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.