1Samisoni adapita ku Timna ndipo kumeneko adaonako mtsikana wachifilisti.
2Atabwerera kwao adakauza bambo ndi mai wake kuti, “Ku Timna ndaonako mtsikana wachifilisti. Mukanditengere ameneyo, ndidzamkwatire.”
3Koma bambo ndi mai wake adamufunsa kuti, “Kodi palibe mkazi woti ungakwatire pakati pa ana a achibale akoŵa kapena pakati pa anthu a mtundu wathu, kuti uzikatenga mkazi pakati pa Afilisti, anthu osaumbalidwa?” Koma Samisoni adauza bambo wake kuti, “Ine ndiye kanditengereni yemweyo, pakuti ndiye ndamkonda kwambiri.”
4Bambo ndi mai wake sankadziŵa kuti zimenezo zinali zochokera kwa Chauta, pakuti Chauta ankafunafuna poŵapezera chifukwa Afilistiwo. Nthaŵi imeneyo nkuti Afilisti akulamulira Aisraele.
5Tsono Samisoni adapita ku Timna pamodzi ndi bambo ndi mai wake. Atafika ku minda yamphesa ya ku Timna, Samisoni adamva mwanawamkango akumdzumira.
6Pamenepo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni ndi kumsandutsa wankhongono. Motero ngakhale analibe chida m'manja, Samisoni adakadzula mkangowo, monga momwe munthu amakadzulira kamwanakambuzi. Koma sadauze bambo kapena mai wake zimene adachitazo.
7Tsono Samisoni adapita kukalankhula naye mtsikana uja, ndipo adamkonda kwambiri mtsikanayo.
8Patapita kanthaŵi Samisoni adabwerera kudzamtenga mtsikanayo. Pa njira adapatuka kukaona mkango adaaupha uja. Adangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake.
9Samisoni adafula njuchizo, natenga uchi m'manja ndi kumapita naadya. Atafika kwa bambo ndi mai wake, adaŵapatsako uchiwo, iwo naadya. Koma sadaŵauze kuti uchiwo adaufula mu mkango wakufa.
10Bambo wakeyo adapita kunyumba kwa mkazi uja, ndipo Samisoni adakonza phwando kumeneko, pakuti ndi m'mene ankachitira anyamata.
11Pamene anthu adamuwona, adabwera ndi anyamata makumi atatu kuti akhale naye.
12Samisoni adaŵauza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi! Mukandiwuza tanthauzo lake, asanapite masiku asanu ndi aŵiri a phwando, ndidzakupatsani zovala zabafuta makumi atatu ndiponso zovala za tsiku lachikondwerero makumi atatu.
13Koma mukalephera kundiwuza tanthauzo lake, mudzandipatsa ndinu zovala zabafuta makumi atatu, ndiponso zovala za tsiku lachikondwerero makumi atatu.” Iwo adamuyankha kuti, “Tiphere mwambiwo, tiwumve.”
14Tsono adaŵauza kuti,
“M'chodya zinzake mudatuluka chakudya.
M'champhamvu mudatuluka chozuna.”
Pa masiku atatu, anthuwo sadathe kuumasula mwambiwo.
15Tsiku lachinai lake iwo adauza mkazi wa Samisoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako, kuti atiwuze tanthauzo lake la mwambi uja, mwinamwina tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya bambo wako. Monga inu mwatiitana kuno kuti mutisandutse osauka?”
16Choncho mkazi wa Samisoni adayamba kulira pamaso pa mwamuna wake namuuza kuti, “Inu mumadana nane, simundikonda konse. Mwaŵaphera mwambi anthu a m'dziko mwangaŵa, koma ine osandiwuzako tanthauzo lake.” Apo Samisoni adamuuza kuti, “Ona, ngakhale bambo wanga ndi mai wanga sindidaŵauze, ndiye ndingauze iweyo?”
17Mkaziyo ankangomulirira masiku onse asanu ndi aŵiri aphwandowo. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adamuuza, chifukwa chakuti adaamkakamiza kwambiri. Pompo mkaziyo adakauza anthu a m'dziko mwake aja tanthauzo la mwambiwo.
18Choncho anthu amumzinda aja adauza Samisoni pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri dzuŵa lisanaloŵe, kuti,
“Nchiyani chozuna kuposa uchi?
Nchiyani champhamvu kuposa mkango?”
Samisoni adaŵauza kuti,
“Mukadapanda kulima ndi msotiwang'ombe wanga,
simukadatha kumasula mwambi wangawu.”
19Apo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni mwamphamvu ndipo Samisoniyo adapita ku Asikeloni nakapha anthu makumi atatu am'mudzimo ndipo adatenga zovala zao za tsiku lachikondwerero, nazipereka kwa amene adamasula mwambi aja. Ndipo adabwerera ku nyumba ya bambo wake ali wokwiya kwambiri.
20Nthaŵi yomweyo mkazi wa Samisoni uja bambo wake adamkwatitsa kwa mnzake wa Samisoniyo amene adaali mnzake womuperekeza paukwati paja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.