1Elisa adayankha nati, “Mverani, zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha ku Samariya’ ”
2Tsono phungu wokhulupirika wa mfumu adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Koma Elisa adati, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.”
Akhate aulula za kuthaŵa kwa Asiriya3Nthaŵi imeneyo panali anthu akhate anai amene ankakhala pa chipata. Iwowo adayamba kufunsana kuti, “Chifukwa chiyani tikungotambalala pano kumangodikira imfa?
4Tikati tiyeni tiloŵe mumzindamu, njala ili m'menemo kumene, ndiye tikaferamo. Komanso tikangotambalala pompano, tifabe. Tsono tiyeni tingopita ku zithando za Asiriya. Akatileka ndi moyo, chabwino, koma akatipha, palibe kanthu.”
5Motero adanyamuka ndi chisisira kupita ku zithando za Asiriya. Koma atafika ku malire a zithando za Asiriya, adaona kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe.
6Chauta anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lankhondo pakati pa ankhondo a Asiriya. Ndiye iwowo adayamba kuuzana kuti, “Tamvani phokosolo, mfumu ya ku Israele yalemba mafumu a Ahiti ndi a Aejipito kuti adzatithire nkhondo!”
7Motero adathaŵa ndi chisisila, nasiya mahema, akavalo, abulu ndiponso katundu wao yense monga momwe adaaliri, nathaŵa kuti apulumutse moyo wao.
8Choncho akhate aja atafika ku malire a zithandozo, adakaloŵa mu hema limodzi, ndipo adadya ndi kumwa. Atatero adatengako siliva, golide ndi zovala, nakazibisa. Pambuyo pake adabwerera nakaloŵa mu hema linanso, natengamo zinthu, nkukazibisanso.
9Kenaka akhate aja adayamba kuuzana kuti, “Ife sitikuchita bwinotu pamenepa. Lero ndilo tsiku limene tili ndi uthenga wabwino kwambiri! Tikakhala chete ndi kumadikira mpaka m'maŵa, tidzalangidwa. Nchifukwa chake tsono tiyeni tikauze nduna za mfumu.”
10Motero adapita ku Samariya nakaitana alonda a pa chipata cha mzinda naŵauza kuti, “Ife tidaapita ku zithando za Asiriya, ndipo tidangoona kuti kulibe munthu ndi mmodzi yemwe. Ngakhale kumva mau sitidamve, koma tidangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire, ndiponso mahema monga momwe adaaliri.”
11Tsono alonda apachipata aja adalengeza uthengawo ndipo okhala kunyumba kwa mfumu adaumva.
12Pamenepo mfumu idadzuka usiku nikauza nduna zake kuti, “Ndikuuzeni zimene Asiriya atikonzera. Iwowo akudziŵa kuti ife tili ndi njala. Nchifukwa chake atuluka m'zithando kuti akabisale ku thengo. Choncho tikangotuluka mumzinda muno, iwowo atigwira amoyo ndipo aloŵa mumzinda muno.”
13Koma mmodzi mwa nduna zake adati, “Anthu a mumzinda muno posachedwa adzatsirizikanso monga Aisraele onse amene afa kaleŵa. Ndiye ife tiyeni tisankhe ena kuti atenge akavalo asanu amene atsalawo, tiŵatume kuti akaone.”
14Motero adasankha anthu aŵiri okwera pa akavalo, ndipo mfumuyo idaŵatuma kuti akalondole gulu la ankhondo la Asiriya. Idati, “Pitani mukaone chimene chachitika.”
15Anthu aja adaŵalondola Asiriya mpaka ku Yordani. Ndipo ndithu m'njira monse ankapeza zovala zili mbwee ndiponso katundu amene Asiriya ankapita nataya chifukwa cha kuthaŵa mofulumira. Pomwepo amithengawo adabwerera, nakauza mfumu.
16Tsono anthu a mu Samariya adatuluka nakafunkha ku zithando za Asiriya. Motero makilogramu atatu a ufa wosalala ankaŵagulitsadi pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele ankaŵagulitsanso chimodzimodzi potsata m'mene adaanenera Chauta.
17Pamene zinkachitika zimenezi, nkuti mfumu itaika phungu wake wokhulupirika uja kuti akhale wolamulira pa chipata. Koma anthu adapondereza phunguyo kuchipata kuja, kotero kuti adafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu adaanenera pamene mfumu idaapita kukamuwona.
18Paja mneneri Elisa adaauza mfumu kuti, “Makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino ku chipata cha Samariya.”
19Pamenepo phungu wokhulupirika uja adaayankha Elisa munthu wa Mulungu uja, kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Apo mpamene Elisa adaamuuza kuti, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.”
20Motero zidamchitikiradi, pakuti anthu adampondereza pa chipata ndipo adafera pomwepo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.