1Mukadzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo,
2Eks. 23.19 aliyense mwa inu pa zokolola zonse zoyamba zimene adazipeza m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, atengeko zina ndi kuziika m'dengu, ndipo apite nazo ku malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azidzapembedzerako.
3Apite kwa mkulu wa ansembe amene ali pa ntchito nthaŵi imeneyo, ndipo amuuze kuti, “Tsopano ndadziŵadi kuti Chauta, Mulungu wanga, wandiloŵetsa m'dziko limene adalonjeza makolo athu kuti adzatipatsa ife.”
4Wansembeyo ndiye amene adzakulandireni dengulo ndi kuliika patsogolo pa guwa la Chauta, Mulungu wanu.
5Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, muzidzanena kuti, “Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda, amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko, anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu ndi wamphamvu.
6Aejipito adatichita zankhanza ndi kutizunza potigwiritsa ntchito mwaukapolo.
7Pamenepo ife tidalirira Chauta, Mulungu wa makolo athu, kuti atithandize. Iyeyo adatimva, ndipo adaona kusauka kwathu, ntchito yolemetsa imene iwo aja ankatigwiritsa, ndiponso moyo wathu wopsinjidwawo.
8Mwa mphamvu zake zazikulu ndiponso ndi dzanja lake lotambalitsa, Chauta adatitulutsa ku Ejipito. Padaoneka zozizwitsa ndi zizindikiro, ndipo padachitika zinthu zoopsa zambiri.
9Potsiriza adatifikitsa kuno, natipatsa dziko lino, dziko lamwanaalirenji.
10Motero tsopano, ndikubwera kwa Chauta ndi gawo la zokolola zoyamba za m'dziko limene wandipatsa.” Apo mutatula pansi dengulo pamaso pa Mulungu, mumpembedze pomwepo.
11Kondwani popeza kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zabwino, inu ndi a m'banja mwanu. Mukondwe inu ndi Alevi, ndiponso alendo amene mumakhala nawo.
12 Deut. 14.28, 29 Chaka chachitatu chilichonse muzipereka chopereka chachikhumi cha zokolola zanu kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, kuti kumizinda kumene amakhala iwoŵa, adzakhale ndi chakudya chokwanira. Mutachita zimenezi,
13munene kwa Chauta kuti, “Palibe nchimodzi chomwe chopereka chachikhumi chimene chatsalako m'nyumba mwanga. Zonse ndapereka kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, monga mudandilamulira. Sindidanyoze kapena kuiŵalapo malamulo anu ndi limodzi lomwe.
14Pa za chachikhumi sindidadyepo nchimodzi chomwe pamene ndinkalira maliro. Pamene ndinali woipitsidwa pa zachipembedzo, sindidagwirepo nchimodzi chomwe. Ndipo sindidaperekepo nchimodzi chomwe kuperekera anthu akufa. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndakumverani. Zonse zimene mudalamula za chopereka chachikhumi ndachita.
15Yang'anani pansi kuchokera kumwambako ku malo anu oyera, ndipo mudalitse anthu anu Aisraele. Mudalitsenso dziko ili lamwanaalirenji limene mwatipatsali, monga momwe mudalonjezera makolo athu.”
Aisraele ndi anthu ake a Chauta16Chauta, Mulungu wanu, akukulamulani lero lino kuti mumvere malangizo ndi malamulo ake. Tsono muŵamveredi ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
17Lero mwamdziŵa Chauta kuti ndi Mulungu wanu. Mwalonjeza kumvera Iyeyo, kusunga malangizo ndi malamulo ake, ndi kuchita zonse zimene akulamulani.
18Eks. 19.5; Deut. 4.20; 7.6; 14.2; Tit. 2.14; 1Pet. 2.9 Lero Chauta wakulandirani ngati anthu ake, monga momwe adakulonjezerani, malinga nkusunga malamulo ake onse.
19Motero pa matamando, pa mbiri ndi pa ulemerero adzakukwezani kupambana mitundu ina yonse ya anthu imene adailenga, ndipo mudzakhala anthu ake oyera mtima, monga momwe adalonjezera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.