1Tsono Rehobowamu adapita ku Sekemu. Apo nkuti Aisraele onse atapita kale ku Sekemuko, kuti akamulonge ufumu.
2Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, adakali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, Yerobowamu adabwerera kuchokera ku Ejipitoko.
3Anthu adakamuitana. Choncho Yerobowamu pamodzi ndi anthu onse a ku Israele adadza kwa Rehobowamu namuuza kuti,
4“Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipepukitsireko goli lolemetsayo ndi ntchito zoŵaŵazo zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.”
5Rehobowamu adauza anthuwo kuti, “Pitani mukabwerenso kuno patapita masiku atatu.” Choncho anthuwo adachoka.
6Apo mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani, kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?”
7Madodawo adamuuza kuti, “Mukamatumikira bwino anthu ameneŵa nkukhaladi mtumiki wao, muzilankhula nawo mau abwino, ndipo iwowo adzakutumikirani mpaka muyaya.”
8Koma Rehobowamu adanyozera zimene madoda aja adaamlangiza, nakapempha nzeru kwa achinyamata anzake, amene adaakula naye pamodzi namamtumikira.
9Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti tiŵayankhe anthu ameneŵa amene andipempha kuti ‘Tipeputsireniko goli limene bambo wanu adatisenzetsa?’ ”
10Anyamata anzakewo adamuuza kuti, “Anthuwo akupemphani kuti, ‘Bambo wanu adatisenzetsa goli lolemera, koma inu mutipeputsireko.’ Inu tsono mukaŵayankhe kuti, ‘Chala changa chakaninse nchachikulu kupambana chiwuno cha bambo wanga!
11Ndiye kuti bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, kuyambira pano ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.’ ”
12Tsono Yerobowamu pamodzi ndi anthu onse adabwera kwa Rehobowamu mkucha wake, monga momwe mfumu idaanenera kuti, “Mubwerenso kuno mkucha.”
13Ndiye mfumuyo idaŵayankha anthuwo mwankhanza. Idanyozera malangizo a madoda aja,
14nilankhula nawo anthuwo potsata malangizo a anyamata anzake, nkunena kuti, “Bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, koma ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.”
15Choncho mfumuyo sidamvere pempho la anthuwo, pakuti Chauta anali atazikonzeratu zinthuzo, kuti zichitikedi zimene adaalankhula ndi Yerobowamu, mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
16 2Sam. 20.1 Tsono Aisraele onse akumpotowo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha mfumuyo kuti,
“Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide?
Sitingayembekeze choloŵa chilichonse
m'banja la mwana wa Yese.
Ndiye inu Aisraele, bwererani ku mahema kwanu!
Tsopano iwe mwana wa Davide,
udziwonere wekha pa banja lako.”
Choncho Aisraelewo adachoka napita ku nyumba zao.
17Koma Rehobowamu adakhala akulamulirabe Aisraele enawo okhala m'mizinda ya Yuda.
18Tsono mfumu Rehobowamu adatuma Adoramu, amene ankayang'anira ntchito yathangata, koma Aisraele onse adamponya miyala mpaka kumupha. Pamenepo mfumu Rehobowamu adakwera msangamsanga pa galeta, nathaŵira ku Yerusalemu.
19Motero Aisraele akumpoto adakhala akupandukira banja la Davide mpaka lero lino.
20Tsono a ku Israele onse atamva kuti Yerobowamu wabwerera kuchokera ku Ejipito, adatumiza mau okamuitana kuti afike ku msonkhano. Kumeneko adamlonga ufumu wolamulira a ku Israele onse. Padaalibe wa ku Israele ndi mmodzi yemwe amene ankatsata ulamuliro wa banja la Davide, kupatula fuko la Yuda lokha.
21Tsono Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, adasonkhanitsa ankhondo 180,000 a fuko la Yuda ndi la Benjamini ndi cholinga chakuti akamenyane ndi mafuko a ku Israele, kuti choncho amubwezere Rehobowamu ufumu wake.
22Koma Mulungu adadza kwa Semaya, mneneri wake, namlamula kuti, “Ukauze
23Rehobowamu, mwana wa Solomoni, mfumu ya ku Yuda, ndiponso anthu onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini kuti,
24‘Ine Chauta ndikuti musapite kukamenyana ndi abale anu a ku Israele. Aliyense abwerere kwao, poti zimene zachitikazi zachokera kwa Ine.’ ” Anthuwo adamvera mau a Chauta, nabwerera kwao monga momwe Chauta adaŵalamulira.
Yerobowamu asiya Mulungu25Yerobowamu, mfumu yakumpoto, adamanganso mzinda wa Sekemu ku dziko la mapiri la Efuremu nakhala kumeneko. Kuchokera kumeneko adapita kukamanganso mzinda wa Penuwele.
26Yerobowamuyo ankaganiza mumtima mwake kuti, “Monga m'mene zilirimu, ufumu udzabwereranso ku banja la Davide.
27Anthu ameneŵa akamapita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, mitima yao idzabwerera kwa mbuyao Rehobowamu, mfumu ya ku Yuda, ndipo adzandipha.”
28Eks. 32.4 Motero mfumuyo itaganizaganiza pa zimenezi, idapanga mafano aŵiri a anaang'ombe agolide. Tsono idauza anthu kuti, “Inu anthu a ku Israele, ku Yerusalemu mwakhala mukupitako nthaŵi yaitali. Tsopano milungu yanu ndi iyi imene idakutulutsani ku dziko la Ejipito.”
29Pamenepo Yerobowamu adatenga fano lina nkuliika ku Betele, lina nkuliika ku Dani.
30Ndipo zimenezi zidachimwitsa a ku Israele, poti anthuwo ena ankapita kukapembedza fano la ku Betele, ena ankakapembedza fano la ku Dani.
31Yerobowamu adamanganso nyumba pa malo achipembedzowo nasankha ansembe pakati pa anthu amene sanali Alevi.
32Lev. 23.33, 34 Ndipo Yerobowamu adakhazikitsa tsiku lachikondwerero, pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, lofanafana ndi tsiku lachikondwerero limene ankachita ku Yuda, napereka nsembe pa guwa nthaŵi imeneyo. Adachita zimenezi ku Betele, namapereka nsembe kwa mafano a anaang'ombe, amene iyeyo adapanga. Ndipo ku Beteleko adaikako ansembe pa malo achipembedzo amene adamanga.
33Yerobowamuyo ankapita ku guwa limene adamanga, pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, mwezi umene iye yekha adausankha. Motero Yerobowamu adalamula kuti pakhale tsiku lachikondwerero la Aisraele, ndipo iye yemwe adapita kukapereka nsembe yofukiza lubani pa guwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.