2 Ako. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Nchifukwa chake ndidatsimikiza kuti ndisachite ulendo winanso wopweteka wobwera kwanuko.

2Ngati ndine amene ndikukupweteketsani mtima, nanga ineyo adzandisangalatsa ndani, kodi si yemweyo amene ndidampweteketsa mtima.

3Nchifukwa chake ndidakulemberani kalata ija. Sindidafune kudza kwanuko, kuwopa kuti inuyo oyenera kundisangalatsanu mungandipweteketse mtima. Ndidaadziŵiratu kuti ine ndikamakondwa, nonsenunso mumakondwa.

4Pamene ndidakulemberani kalata ija, mtima wanga unali wovutika ndi wopsinjika ndithu, ndipo ndinkalira misozi. Sindidafune kukupweteketsani mtima, koma makamaka ndinkafuna kuti mudziŵe kuti ndimakukondani kwambiri.

Paulo akhululukira iye amene adaalakwa

5Ngati wina aliyense adachita kanthu kolasa mtima, si ineyo amene adalasa mtima, koma pang'ono ponse adalasako nonsenu, kunenatu mosakulitsa nkhani.

6Munthu woteroyo, pafupi nonse mwamtsutsa, choncho chilangocho nchokwanira.

7Tsono makamaka nkwabwino mumkhululukire ndi kumlimbitsa mtima, kuwopa kuti angamve chisoni chachikulu chomtayitsa mtima kotheratu.

8Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mumtsimikizirenso kuti mumamkonda ndithu.

9Pamene ndinkakulemberani kalata ija, cholinga changa chinali chakuti ndikuyeseni, ndi kuwona ngati mudzandimvera pa zonse.

10Mukakhululukira munthu, inenso ndimkhululukira. Ngati ine ndakhululukira, patakhala kanthu koti ndakhululukira, ndiye kuti ndakhululukira chifukwa cha inu pamaso pa Khristu.

11Cholinga chake nkuti Satana asatichenjerere, paja tikudziŵa njira zake.

Za nkhaŵa ya Paulo ku Troasi

12 Ntc. 20.1 Pamene ndidafika ku Troasi kuti ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Khristu, ndidapeza Ambuye atanditsekulira kale pa khomo kuti ndikagwire ntchito kumeneko.

13Komabe mumtima mwanga munalibe mtendere, chifukwa sindidampeze Tito, mbale wanga. Tsono ndidatsazikana ndi anthu akumeneko nkupita ku Masedoniya.

Khristu amapambanitsa anthu ake

14Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.

15Zoonadi tili ngati fungo labwino la Khristu lokomera Mulungu, pakati pa anthu amene akupulumuka ndi amene akutayika.

16Kwa amene akutayika, fungoli ndi la imfa, ndipo limaŵapha. Koma kwa amene akupulumuka, fungoli ndi la moyo, ndipo limaŵapatsa moyo.

Nanga ndani angaithe ntchito yotere?

17Ifetu sitili ngati anthu ena ambiri amene amangochita malonda ndi mau a Mulungu. Koma, popeza kuti tili mwa Khristu, ngati anthu otumidwa ndi Mulungu, timalankhula moona, molingana ndi kufuna kwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help