1Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aisraele kuti pa zonse zimene Chauta adaletsa, munthu aliyense akachimwapo mosadziŵa, pochita kanthu kena kalikonse koletsedwa, azichita izi:
3wochimwayo akakhala wansembe wodzozedwa, pakutero wausandutsa wopalamula mpingo wonse, tsono azipereka kwa Chauta ng'ombe yaing'ono yamphongo yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo ake.
4Wansembe abwere ndi ng'ombeyo pa khomo la chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo aiphe pamaso pa Chauta.
5Kenaka wansembe wodzozedwayo atengeko magazi a ng'ombeyo ndi kubwera nawo ku chihema chamsonkhano.
6Apo aviike chala chake m'magazi, ndi kuwaza magaziwo kasanu ndi kaŵiri patsogolo pa nsalu yochinga malo oyera pamaso pa Chauta.
7Pambuyo pake wansembe apakeko magaziwo pa nyanga za guwa la m'chihema chamsonkhano lofukizirapo lubani wonunkhira fungo lokoma pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala a ng'ombeyo aŵathire pa tsinde la guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.
8Tsono mafuta onse a ng'ombe yamphongo yoperekera nsembe yopepesera machimoyo, aŵachotse pamodzi ndi mafuta okuta matumbo, ndiponso mafuta ena onse okhala pamatumbopo.
9Achotsenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu za mafuta akuchiŵindi ochotsa pamodzi ndi imso zija,
10monga momwe amazichotsera ku ng'ombe yopereka pa nsembe yachiyanjano. Tsono wansembeyo atenthe zonsezo pa guwa la nsembe zopsereza.
11Koma chikopa cha ng'ombe yamphongoyo, pamodzi ndi mnofu wake, mutu wake, miyendo yake, matumbo ake ndi ndoŵe yake,
12kungoti ng'ombe yonseyo, atuluke nayo kunja kwa mahema, ku malo oyeretsedwa kumene amatayako phulusa, ndipo pamalo pomwepo aitenthere pa moto wankhuni.
13“Ngati mpingo wonse wa Aisraele uchimwa mosachitira dala, nuchita zimene Chauta amaletsa, ngakhale uli wosadziŵako, ngwopalamula ndithu.
14Tsono tchimo lakelo nkudziŵika, mpingo wonsewo upereke ng'ombe yaing'ono yamphongo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo abwere nayo pa khomo la chihema chamsonkhano.
15Apo atsogoleri a mpingo asanjike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Chauta, ndipo aiphe pamaso pa Chauta.
16Wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ng'ombe yamphongoyo ndi kubwera nawo ku chihema chamsonkhano.
17Pamenepo wansembeyo aviike chala chake m'magazi, ndipo pamaso pa Chauta awaze magaziwo kasanu ndi kaŵiri patsogolo pa nsalu yochinga.
18Pambuyo pake magaziwo aŵapake pa nyanga za guwa limene lili m'chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala aŵathire patsinde pa guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.
19Kenaka mafuta ake onse aŵachotse ndi kuŵatenthera pa guwa.
20Umu ndimo m'mene ng'ombe yamphongo aichitire. Monga adachitira ndi ng'ombe yamphongo yopereka pa nsembe yopepesera machimo, ndimo aichitirenso imeneyi. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimowu, mpingowo udzakhululukidwa.
21Tsono ng'ombeyo aitulutsire kunja kwa mahema ndi kuitentha monga momwe adachitira ndi yoyamba ija. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo, yoperekera mpingo wonse.
22“Wolamula akachimwa mosadziŵa, kuchimwira Chauta, Mulungu wake, pa chinthu choletsedwa, napalamula pakutero,
23pambuyo pake ena nkumudziŵitsa za tchimo lakelo, iyeyo apereke nsembe ya tonde wopanda chilema.
24Tsono wolamulayo asanjike dzanja lake pamutu pa tondeyo ndi kumupha pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza pamaso pa Chauta. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo.
25Wansembe atengeko magazi a tondeyo ndi chala chake, aŵapake pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndi kuthira magazi otsalowo patsinde pa guwa lomwelo.
26Kenaka mafuta ake onse aŵatenthere pa guwa, monga momwe amachitira ndi mafuta a nsembe yachiyanjano. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo a wopalamula uja, munthuyo adzakhululukidwa.
27 Num. 15.27, 28 “Ngati munthu wamba aliyense achimwa mosadziŵa, pochita china chilichonse chimene Chauta amaletsa, napalamula pakutero,
28tchimo lakelo akalizindikira, apereke nsembe ya mbuzi yaikazi yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo.
29Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa mbuzi ya nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aiphere pa malo amene amaperekera nsembe yopsereza.
30Atatero, wansembe atengeko magazi ndi chala chake, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndipo magazi otsalawo aŵathire patsinde pa guwa lomwelo.
31Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta a nsembe yachiyanjano, ndipo wansembe aŵatenthe pa guwalo, kuti atulutse fungo lokomera Chauta. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo a munthu wamba uja, munthuyo adzakhululukidwa.
32“Ngati munthu abwera kudzapereka nkhosa ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa yake ikhale yaikazi, yopanda chilema.
33Ndipo asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosa ya nsembe yopepesera machimoyo, ndi kuiphera pa malo amene amaphera nsembe yopsereza.
34Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a nkhosayo ndi chala chake, ndipo aŵapake pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndi kuthira magazi otsalawo patsinde pa guwalo.
35Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta a nkhosa yoperekera nsembe yachiyanjano. Ndipo aŵatenthe pa guwa, pamodzi ndi nsembe zina zopsereza pa moto, zopereka kwa Chauta. Umu ndimo m'mene wansembe azichitira mwambo wopepesera tchimo la munthu, ndipo munthuyo adzakhululukidwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.