Mk. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu aloŵa ndi ulemu mu Yerusalemu(Mt. 21.1-11; Lk. 19.28-40; Yoh. 12.12-19)

1Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankayandikira ku Yerusalemu, kufupi ndi ku Betefage ndi Betaniya, midzi ya ku Phiri la Olivi, Iye adatuma aŵiri mwa ophunzirawo,

2naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukangoloŵamo, mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule nkubwera naye.

3Wina akakakufunsani kuti, ‘Inu, nchiyani chimenecho?’ Inu mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito, akangothana naye amtumiza konkuno nthaŵi yomweyo.’ ”

4Ophunzira aja adapitadi, nakapeza mwanawabuluyo ali chimangirire pa khomo m'mbali mwa mseu, ndipo adayamba kummasula.

5Anthu amene adaali pamenepo adaŵafunsa kuti, “Inu nchiyani chimenecho, buluyo mukummasuliranji?”

6Ophunzirawo adaŵayankha monga momwe adaaŵauzira Yesu. Tsono anthuwo adaŵalola kuti ammasule.

7Ophunzira aja adabwera naye mwanawabuluyo kwa Yesu. Adayala zovala zao pamsana pa bulu uja, Yesu nkukwerapo.

8Anthu ambiri ankayala zovala zao mu mseu, ena nkumayalika nthambi zamasamba zomwe ankakazithyola ku thengo.

9

16Sadalolenso kuti wina aliyense azidutsa m'mabwalo a Nyumbayo atasenza chinthu ai.

17Yes. 56.7; Yer. 7.11Pambuyo pake adayamba kuŵaphunzitsa naŵauza kuti, “Paja Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”

18Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo atamva zimenezi, adayamba kufunafuna njira yoti amuphere. Pakutitu ankachita naye mantha poona kuti anthu onse ankadabwa nazo zimene Iye ankaphunzitsa.

19Kutayamba kuda, Yesu ndi ophunzira ake adatulukamo mumzindamo.

Phunziro la mkuyu wotembereredwa uja(Mt. 21.20-22)

20M'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, iwo akuyenda mu mseu, adaona mkuyu uja waumiratu wonse ndi mizu yomwe.

21Apo Petro adakumbuka zijazi, ndipo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, taonani, mkuyu uja mudautembererawu wauma.”

22Yesu adaŵayankha kuti, “Muzikhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.

23Mt. 17.20; 1Ako. 13.2Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wolamula phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ atanena ndi mtima wosakayika, nakhulupirira ndithu kuti zimene akunenazo zichitikadi, ndithu zidzachitikadi monga momwe waneneramo.

24Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.

25Mt. 6.14, 15Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.”

[

26“Koma ngati inu simukhululukira anzanu, Atate anunso amene ali Kumwamba sadzakhululukira machimo anu.”]

Afunsa Yesu za ulamuliro wake(Mt. 21.23-27; Lk. 20.1-8)

27Yesu adafikanso ku Yerusalemu. Tsono pamene Iye ankangodziyendera m'Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti,

28“Kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?”

29Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzeni kumene ndidatenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.

30Kodi Yohane kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu? Tandiyankhani.”

31Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono simudamkhulupirire?’

32Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, apo ndiye ainso.” Adaatero chifukwa choopa anthu, pakuti anthu onse ankati Yohane anali mneneri weniweni.

33Ndiye adangomuyankha Yesuyo kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa.” Apo Iye adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help