1Koma Aisraele ena sadamvere lamulo la Chauta loti asatenge kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono amene adaagwinyako zinthuzo, anali Akani. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda. Choncho Chauta adakwiyira Aisraele onse kwambiri.
2Atagonjetsa Yeriko, Yoswa adatuma anthu ena kuti akazonde mzinda wa Ai. Mzinda umenewu unali kuvuma kwa Betele, pafupi ndi Betaveni. Ataŵatuma kuti akazonde mzindawo, anthu aja adapitadi nazonda mzinda wa Ai.
3Atabwerera kwa Yoswa, anthuwo adamuuza kuti, “Sikofunikira kuti tipite tonse kumeneko. Ingotumani anthu zikwi ziŵiri kapena zitatu kuti akathire nkhondo mzinda wa Ai. Musatume anthu onse kumeneko poti si mzinda waukulu.”
4Motero Yoswa adangotuma anthu ngati zikwi zitatu. Koma tsono anthu a ku Ai adapirikitsa Aisraelewo.
5Anthu a ku Ai adathamangitsa Aisraele kuchokera ku chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya. Aisraele okwanira ngati 36 adaphedwa, makamaka pamene ankatsika phiri. Motero Aisraele onse adataya mtima, ndipo adachita mantha kwambiri.
6Yoswa atamva zimenezi, adamva chisoni kwambiri, ndipo adang'amba zovala zake, nagwada patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta lija. Atsogoleri onse a Aisraele nawonso adadzigwetsa pansi pa malo omwewo mpaka madzulo, atadzola fumbi kumutu, kusonyeza chisoni chaocho.
7Tsono Yoswa adati, “Kalanga ine Chauta! Chifukwa chiyani mudatiwolotsa Yordani? Kani mudatipereka m'manja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Bwanji osangotileka kuti tikhale tsidya ilo la Yordani?
8Nanga ndinene chiyani tsopano, Chauta, poona kuti Aisraele athamangitsidwa ndi adani ao chotero?
9Akanani ndi anthu ena onse okhala m'dziko muno adzamva zimenezi, ndipo adzatizinga ndi kutipha tonse. Kodi pamenepa inu mudzachitapo chiyani kuti ulemu wanu usaonongeke?”
10Chauta adamuuza Yoswa kuti, “Dzuka, chifukwa chiyani wagwada pansi chotere?
11Aisraele ena adachimwa. Chipangano chija ndidapangana nawochi sadasunge. Zinthu zija ndidaŵauza kuti aonongezi, adagwinyako. Adabako, ndi kunenanso bodza, namaika zinthu zakubazo pakati pa zinthu zao.
12Nchifukwa chake Aisraele sangathe kulimbana ndi adani ao. Athaŵa pamaso pa adani ao chifukwa choti iwowo ngoyenera kuwonongedwa. Sindidzakhala nawonso mpaka utaononga zinthu zimene ndidakulamula kuti usatenge.
13Nyamuka, ukalamule anthu kuti adzipatule, kuti akonzekere kuwonana ndi Ine maŵa, chifukwa Ine Mulungu wa Aisraele ndidzaŵauza kuti, ‘Inu Aisraele, zinthu zija ndidaakuuzani kuti muwonongezi, zili pakati panu. Inu simungalimbe polimbana ndi adani anu, mpaka zinthu zimenezi mutachotsa.’
14Motero maŵa m'maŵa, mutulukire poyera nonsenu, fuko limodzilimodzi. Fuko limene Ine Chauta ndidzaliloze lidzabwera patsogolo, mbumba imodziimodzi. Mbumba imene ndidzailoze idzabwera patsogolo, banja limodzilimodzi. Banja limene ndidzaliloze lidzabwera patsogolo, munthu mmodzimmodzi
15Yemwe adzapezeke ndi zinthu zimenezo, adzatenthedwa pamodzi ndi banja lake lonse ndi zonse zomwe ali nazo. Chinthu chimene wachitacho nchoopsa, chifukwa waphwanya pangano lomwe anthu anga adachita ndi Ine.”
16M'maŵa mwake Yoswa adadzuka m'mamaŵa, natulutsa Aisraele onse fuko limodzilimodzi. Fuko la Yuda lidalozedwa.
17Mbumba zonse za fuko la Yuda adazitulutsira poyera, ndipo mbumba ya Zera idagwidwa. Tsono mabanja a Zera adaŵatulutsira poyera, ndipo banja la Zabidi lidagwidwa.
18Pompo Yoswa adatulutsa anthu onse a banja la Zabidi, ndipo Akani adagwidwa. Iyeyo anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda.
19Tsono Yoswa adauza Akani kuti, “Iwe mwana wanga, lemekeza Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo umtamande. Uze tsopano lino zimene wachita. Usati undibisire.”
20Akani adayankha kuti, “Indedi, ine ndidachimwa, ndidachimwira Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo zimene ndidachita ndi izi:
21pakati pa chuma chija, ndidaonapo mwinjiro wokongola wa ku Babiloni, ndi makilogramu aŵiri a siliva ndiponso munsi wa golide wolemera theka la kilogramu. Zonsezi ndidaazikhumba kwambiri, kotero kuti ndidatenga ndithu. Mungathe kuzipeza m'chithando changa m'mene ndidazibisa. Mukapezanso silivayo pansi pa zinthu zinazo.”
22Motero Yoswa adatuma anthu ena kuti apite kuchithandoko, ndipo adakapezadi kuti zonsezo adazibisa kumeneko, ndipo kuti silivayo adamubisadi pansi.
23Adazitulutsa zonsezo m'chithandomo, napita nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraele onse. Ndipo adaziika pamaso pa Chauta.
24Yoswa ndi Aisraele onse adamtenga Akani ndi zinthu zimene adapezeka nazo zija monga silivayo, mwinjiro ndi munsi wa golide uja. Adatenganso ana ake aamuna ndi aakazi omwe, ndi zoŵeta zake, ng'ombe, abulu, nkhosa, ndi hema lake ndi zonse zomwe anali nazo. Zonsezo adapita nazo ku chigwa chotchedwa Akori.
25Tsono Yoswa adati, “Chifukwa chiyani watiputira mavuto otereŵa? Tsopano Chauta ndiye amene adzetse mavuto ameneŵa pa iwe!” Pompo anthu onsewo adamponya miyala Akani, namupha. Adaponya miyala banja lake lonse, mpakanso kulitentha pamodzi ndi zake zonse.
26Adaunjika mulu waukulu wamiyala pa iyeyo, ndipo muluwo ulipo mpaka lero lino. Nchifukwa chake mpaka lero chigwa chimenechi amachitchula kuti “Chigwa cha Mavuto.” Motero mtima wa Chauta udatsika.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.