Owe. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mitundu imene idatsalira m'dzikomo.

1Tsono Chauta adasiya mitundu ina ya anthu, kuti ayese nayo Aisraele, ndiye kuti Aisraele onse amene sadamenye nao nkhondo ku Kanani.

2Chauta ankangofuna kuti mibadwo yonse ya Aisraele idziŵe kumenya nkhondo, ndiponso kuti aphunzitse makamaka amene sadaidziŵe nkhondo nkale lonse.

3Mitunduyo ndi iyi: mafumu asanu a Afilisti, Akanani onse, Asidoni onse ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni, kuyambira ku phiri la Baala-Heremoni mpaka ku mpata wa Hamati.

4Adaŵasiya kuti aziyesa nawo Aisraele, kuti aone ngati Aisraele adzamvera malamulo amene Chauta adaapatsa makolo ao kudzera mwa Mose.

5Choncho Aisraele adakhala pakati pa Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.

6Aisraelewo adayamba kukwatirana ndi anthu a mitundu imeneyo, ndiponso kukwatitsa ana ao kwa amuna a mitundu inayo. Kenaka adayamba kupembedza milungu yao.

Za Otiniyele.

7Aisraele adachita zinthu zoipira Chauta. Adaiŵala Chauta, Mulungu wao, namatumikira mafano a Abaala ndi Asitaroti.

8Nchifukwa chake Chauta adaŵapsera mtima Aisraelewo, naŵagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraele adatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.

9Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa; amene adaŵapulumutsayo ndi Otiniyele, mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe.

10Mzimu wa Chauta udatsika pa iye, ndipo adasanduka mtsogoleri wa Aisraele. Adapita kukamenya nkhondo, ndipo Chauta adapereka Kusani-Risataimu, mfumu ya ku Mesopotamiya, m'manja mwake, namgonjetsa.

11Motero dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai. Pambuyo pake Otiniyele, mwana wa Kenazi, adamwalira.

Za Ehudi.

12Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta. Ndiye Chauta adapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kuti alimbane ndi Aisraele, chifukwa chakuti iwowo adaachita zinthu zoipira Chauta.

13Egiloniyo adamemeza Aamoni ndiponso Aamaleke, napita kukagonjetsa Aisraele. Ndipo adalanda Yeriko, mzinda wamigwalangwa.

14Tsono Aisraele adakhala akapolo a Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, zaka 18.

15Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa. Iyeyu anali Ehudi, mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini, munthu wamanzere. Aisraele ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kudzera kwa Ehudi.

16Tsono Ehudi adasula lupanga lake lakuthwa kuŵiri, kutalika kwake masentimita 50. Ndipo adamangirira lupangalo pa ntchafu yake yakumanja m'kati mwa zovala zake.

17Adapita kukapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, amene anali wonenepa kwambiri.

18Ehudi atamaliza kupereka msonkhowo, adauza anthu onyamula msonkhowo kuti azipita.

19Koma iyeyo adabwerera pa malo a miyala yozokotedwa ku Giligala, ndipo atafika kwa mfumu adati, “Zikomo amfumu, ndimati ndikuuzeni mau achinsinsi.” Pamenepo mfumuyo idalamula atumiki ake kuti akhale chete, niŵatulutsa onsewo.

20Tsono Ehudi adasendera pafupi ndi mfumuyo, iyoyo itakhala yokhayokha m'chipinda cham'mwamba chozizira bwino. Ndipo adati, “Ndili ndi mau ochokera kwa Mulungu oti ndikuuzeni.” Mfumuyo idadzuka pa mpando wake.

21Apo Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, adasolola lupanga pa ntchafu yake yakumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba.

22Lupangalo lidaloŵa ndi chigumbu chomwe, ndipo mafuta adaphimba lupangalo pakuti sadalitulutsenso m'mimbamo, adalisiya litatulukira kumbuyo.

23Ehudi adatulukira m'khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda cham'mwambacho.

24Ehudi atachoka, atumiki a mfumu adabwera. Ataona kuti zitseko za chipinda cham'mwamba nzokhoma, adaganiza kuti, “Kapena mfumu ikudzithandiza m'katimo.”

25Iwo adadikira nthaŵi yaitali, kotero kuti sadaone konse chochita. Koma ataona kuti mfumuyo sidatsekulebe zitseko zija, adatenga kii natsekula zitsekozo, ndipo adangoona mfumu yao ili thasa pansi, itafa.

26Ehudi adathaŵa pamene iwo ankachedwa nkudikira. Adapitirira malo a miyala yozokota ija, nathaŵira ku Seira.

27Atangofika adaimba lipenga m'dziko lamapiri la ku Efuremu. Aisraele onse adatsika pamodzi naye kuchokera ku dziko lamapirilo, iyeyo akuŵatsogolera.

28Adauza anthuwo kuti, “Tiyeni kuno, Chauta wapereka Amowabu, adani anu, m'manja mwanu.” Choncho anthuwo adamtsata nakalanda madooko a Yordani natsekereza Amowabuwo, osalola kuti munthu ndi mmodzi yemwe aoloke.

29Nthaŵi imeneyo adapha Amowabu pafupi 10,000. Anthu onse ophedwawo anali amphamvu ndiponso odziŵa kumenya nkhondo, koma sadapulumukepo ndi mmodzi yemwe.

30Choncho Amowabu adagonjetsedwa ndi Aisraele pa tsiku limenelo. Ndipo dzikolo lidakhala pa mtendere zaka makumi asanu ndi atatu.

Za Samigara.

31Atamwalira Ehudi, padabwera Samigara, mwana wa Anati, amene adapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ng'ombe. Motero iyeyunso adapulumutsa Aisraele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help