1 Eks. 23.4, 5 Mukaona ng'ombe kapena nkhosa ya Mwisraele mnzanu ikusokera, musailekerere. Itengeni, mukampatse mwiniwake.
2Koma ngati mwiniwake kwao nkutali, kapena simumdziŵa, itengeni mupite nayo kwanu, muisunge komweko. Koma mwiniwake akabwera kudzaifunafuna, mumpatse.
3Mukapeza bulu, chovala kapena kanthu kena kalikonse kamene Mwisraele mnzanu wataya, chitani chimodzimodzi, musakalekerere ai.
4Bulu wa Mwisraele mnzanu akagona mu mseu, muutseni. Muchitenso chimodzimodzi ndi ng'ombe yake, musailekerere. Mthandizeni mnzanu kuti adzutse choŵetacho.
5Akazi asamavale zovala za amuna, chimodzimodzi amuna asamavale zovala za akazi. Chauta, Mulungu wanu, amanyansidwa nawo anthu ochita zotere.
6Ngati mupeza chisa cha mbalame mu mtengo kapena pansi, make ali pa mazira, kapena ali ndi tiana take, musaitenge mbalameyo pamodzi ndi tiana take.
7Tianato mungathe kutenga, koma makeyo mloleni apite, kuti mukakhale ndi moyo wabwino ndi wautali.
8Pamene mukumanga nyumba, muwonedi kuti mwamanga kampanda pamwamba kuzungulira mbali zonse zadenga. Apo inuyo simudzazengedwa mlandu wa kukhetsa magazi ngati wina agwa kuchokera pa denga, naphedwa.
9 Lev. 19.19 M'munda wamphesa musabzalemo mbeu ina iliyonse. Ngati mutero, zonse zidzakhala zoletsedwa, mphesazo ndi mbeu zina zomwe.
10Musamange ng'ombe ndi bulu kuti zilimire pamodzi.
11Musamavale nsalu yoombedwa ndi ubweya pamodzi ndi thonje.
12Num. 15.37-41 Sokani mphonje pa ngodya zinai za miinjiro yanu imene mumavala.
Za malamulo a ukwati13Mwina munthu angathe kukwatira mtsikana, namakhala naye ndithu, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna.
14Tsono ayamba kumnenera zabodza zochititsa manyazi ndi kuipitsa mbiri yake ponena kuti, “Mkazi ameneyu sadaoneke ngati namwali wosadziŵa mwamuna pa nthaŵi yomukwatira.”
15Zitatero, makolo a mkaziyo atenge zizindikiro zotsimikizira akuluakulu abwalo am'mudzimo kuti mwana waoyo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ndithu.
16Pamenepo bambo wake wa mtsikanayo aŵauze abwalowo kuti, “Ndidalola mwana wanga wamkazi kuti akwatiwe ndi munthu uyu, koma tsopano akuti sakumufuna.
17Wamnamizira momchititsa manyazi kuti ati sadali namwali wosadziŵa mwamuna pomkwatira. Koma pano tili ndi umboni wotsimikizira kuti mwana wangayu adaali namwali wangwiro ndithu. Onani, zizindikiro zake ndi izi.” Apo adzaonetse chovala cha mkaziyo kwa akuluakuluwo.
18Tsono akuluakulu am'mudzimo amtenge mwamunayo ndi kumkwapula.
19Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula.
20Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo umboni wakuti mtsikanayo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ukusoŵa,
21pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu.
22Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu.
23Tiyese kuti mwagwira munthu mumzinda momwemo akuchita chigololo ndi mnamwali wofunsidwa mbeta, amene sadamdziŵeko mwamuna.
24Muŵatenge onsewo, mupite nawo kunja kwa mzinda, ndipo muŵaphe poŵaponya miyala. Mtsikanayo aphedwe chifukwa ngakhale anali m'mudzi, sadakuwe kuti anthu adzamthandize. Mwamunayo aphedwe chifukwa wachimwa ndi mtsikana wofunsidwa mbeta ndi mnzake. Motero mudzachotsa choipa pakati panu.
25Mwina munthu, kuthengo koteroko, achita kugwirira mtsikana wofunsidwa mbeta nachita naye chigololo momkakamiza. Zikatero, munthu wamwamuna yekhayo ndiye aphedwe.
26Mtsikanayo musamchite kanthu chifukwa choti sadachite tchimo loyenera kufa nalo. Mlandu umenewu ukufanafana ndi wakuti munthu aputa mnzake, namupha.
27Munthuyo wachita kumgwira mtsikanayo nkuchita naye chigololo kuthengo. Ndipo ngakhale adaakuwa, panalibe amene akadampulumutsa.
28 Eks. 22.16, 17 Mwina munthu agwidwa akugwirira mnamwali wosafunsidwa mbeta, amene sadamdziweko mwamuna, nachita naye chigololo momkakamiza.
29Munthuyo alipe bambo wake wa mtsikanayo mtengo wofunsira mbeta, ndiye kuti masekeli asiliva makumi asanu, ndipo amtenge kuti akhale mkazi wake chifukwa choti adamkakamiza kuchita naye chigololo. Tsono pa moyo wake wonse sangathenso kumsudzula.
30 Lev. 18.8; 20.11; Deut. 27.20 Munthu asakwatire mkazi wa bambo wake, kapena kuchita chipongwe chomuvula.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.