1Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti,
“Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.”
2Mapazi athu akhala akuima m'kati mwa zipata zako,
iwe Yerusalemu.
3Yerusalemu adamangidwa bwino,
zigawo zake zonse nzogwirizana pamodzi.
4Kumeneko kumapita mafuko onse,
anthu ake a Chauta,
monga momwe adalamulira Israele
kuti akayamike dzina la Chauta.
5Kumeneko adaikako mipando yaufumu yoweruzira,
mipando yake ya banja la Davide.
6Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti,
“Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu,
zinthu ziziŵayendera bwino.
7Mtendere ukhale m'kati mwa makoma ako,
bata likhale m'nyumba zako zachifumu.”
8Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga
ndidzanena kuti,
“Mtendere ukhaledi m'kati mwako.”
9Chifukwa cha Nyumba ya Chauta, Mulungu wathu,
ndidzakupemphera zabwino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.