1 Ntc. 7.40 Anthu ataona kuti Mose wakhalitsako kuphiri osatsikako, adasonkhana kwa Aroni, ndipo adamuuza kuti, “Tiyeni mutipangire milungu yotitsogolera ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamugwera Moseyo, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito kuja.”
2Tsono Aroni adauza anthuwo kuti, “Vulani nsapule zagolide kukhutu kwa akazi anu, kwa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi omwe, ndipo mubwere nazo kwa ine.”
3Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni.
41Maf. 12.28; Ntc. 7.41 Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.”
5Aroniyo ataona zimenezi, adapanga guwa patsogolo pa mwanawang'ombe wagolideyo. Tsono adalengeza kuti, “Maŵa padzakhala chikondwerero cholemekeza Chauta.”
61Ako. 10.7 Choncho m'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, adapereka nsembe zopsereza, nabweranso ndi nsembe zamtendere. Ndipo anthuwo adakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa, kenaka adayambanso kuvina.
7Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Fulumira, tsika phiri, chifukwa anthu ako amene udaŵatsogolera poŵatulutsa ku Ejipito aja, adziipitsa kwambiri.
8Asiya mwamsanga zonse zija zimene ndidaŵalamula kuti azichita. Adzipangira fano la mwanawang'ombe wa golide wosungunula, ndipo alipembedza ndi kuliphera nsembe, namanena kuti, ‘Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.’ ”
9Ndipo Chauta adaonjeza kuti, “Anthu ameneŵa ndikuŵadziŵa, ngokanika kwambiri.
10Nchifukwa chake tsono, undileke kuti ndiŵaononge chifukwa ndili wokwiya kwambiri, koma iweyo ndidzakusandutsa mtundu waukulu wa anthu.”
11 Num. 14.13-19 Koma Mose adapepesa Chauta wake, nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukukwiyira anthu anu chotere, anthu amene mudaŵatulutsa mu ukapolo ku Ejipito kuja ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu?
12Kodi mukufuna kuti Aejipitowo azidzanena kuti, ‘Adaŵatulutsa ku Ejipito ndi cholinga choipa choti akaŵaphere ku mapiri ndi kuŵaonongeratu pa dziko lapansi?’ Ukali wanu woyaka ngati motowo ubwezeni, ndipo musaŵaononge anthu anu.
13Gen. 22.16, 17; 17.8 Kumbukirani atumiki anu aja Abrahamu, Isaki ndi Israele ndiponso zija mudaŵalonjezazi molumbira pa dzina lanu, pamene mudaŵauza kuti, ‘Ndidzakupatsani zidzukulu zambiri, zochuluka ngati nyenyezi zakuthambo. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonse limene ndidalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lao mpaka muyaya.’ ”
14Choncho Chauta adaleka chilango choopsa chimene adaati agwetsere anthu akewo.
15Mose adabwerera natsika phiri atanyamula miyala iŵiri ija yaumboni, yolembedwa mbali zonse ziŵiri.
16Imeneyi inali ntchito ya Mulungu, ndipo zolembedwazo adaalemba ndi Mulungu mwini mozizokota pamiyalapo.
17Tsono Yoswa adamva anthu akufuula, nauza Mose kuti, “Ndikumva phokoso lankhondo kumahemako.”
18Koma Mose adati, “Phokoso limenelo silikumveka ngati phokoso la opambana pa nkhondo, kapenanso kulira kwa ogonjetsedwa. Ndikumva phokoso la kuimba.”
19Mose atafika pafupi ndi mahema aja, ndi kuwona mwanawang'ombe uja ndi anthu ovina, adakalipa kwambiri. Adaponya pansi miyala inali m'manja mwake ija, naiphwanya patsinde pa phiri paja.
20Pomwepo adakatenga mwanawang'ombe amene Aroni adapanga, namperapera ngati ufa, ndipo adakamtaya m'madzi. Tsono Aisraele aja adaŵamwetsa madziwo.
21Kenaka Mose adafunsa Aroni uja kuti, “Kodi anthu ameneŵa adakuchita zotani iwe, kuti uŵachimwitse koopsa chotere?”
22Aroni adayankha kuti, “Musakwiyire ine mbuyanga. Mumaŵadziŵa anthu ameneŵa kuti ngovuta.
23Iwoŵa adandiwuza kuti, ‘Tipangireni milungu yoti ititsogolere ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamgwera Mose, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito.’
24Tsono ine ndidaŵauza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi golide abwere naye.’ Ndipo amene anali nazo zinthu zopangidwa ndi golide adandipatsa. Ndidaziponya pa moto, ndipo ndidapanga fano la mwanawang'ombe lija.”
25Mose adaonadi kuti anthuwo ngosokonezeka, (chifukwa Aroni adaaŵalekerera, mpaka iwo kusanduka anthu oŵanyodola pakati pa adani ao).
26Moseyo adaimirira pa chipata cha mahema aja ndipo adafuula mokweza nafunsa kuti, “Kodi ndani akufuna Chauta? Bwerani kuno.” Pompo Alevi onse adadzasonkhana kwa iye,
27ndipo Mose adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Aliyense mwa inu atenge lupanga, ndipo mupite ku mahema ndi kuloŵa m'zipata zonse. Aliyense mwa inu akaphe mbale wake kapena bwenzi lake kapena mnansi.’ ”
28Aleviwo adachitadi monga momwe Mose adaŵalamulira, ndipo amuna 3,000 adaphedwa pa tsiku limenelo.
29Apo Mose adauza Aleviwo kuti, “Lero lino mwadzipatula nokha kuti mukhale ansembe otumikira Chauta, pakupha ana anu ndi abale anu omwe. Motero Chauta akudalitsani lero.”
30M'maŵa mwake Mose adauza anthu kuti, “Inu mudachimwa koopsa. Koma tsopano ndidzapita kwa Chauta ku phiri, ndipo nditakupemphererani, kapena angathe kukukhululukirani machimo anu.”
31Tsono Mose adabwerera kwa Chauta nakanena kuti, “Anthu aŵa adachimwa koopsa. Adadzipangira milungu yagolide.
32Mas. 69.28; Chiv. 3.5 Koma tsopano, chonde muŵakhululukire machimo ao. Mukapanda kuŵakhululukira, chonde mufafanize dzina langa m'buku m'mene mudalemba.”
33Apo Chauta adauza Mose kuti, “Yekhayo amene wandilakwira Ine, ndiye amene ndidzachotse dzina lake m'buku langa.
34Tsopano pita uŵatsogolere anthuwo ku malo amene ndidakuuza. Kumbukira kuti mngelo wanga adzakutsogolera, koma tsiku likubwera limene ndidzaŵalange iwowo chifukwa cha machimo ao.”
35Motero Chauta adatumiza nthenda pa anthuwo, chifukwa choti adakakamiza Aroni kuti aŵapangire fano la mwanawang'ombe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.