1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, ulose ndipo ulengeze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi:
“ ‘Pepani, tsiku latsoka lafika!
3Ndithudi layandikira,
tsiku la Chauta lili pafupi.
Tsiku lamitambo,
tsiku la kutha kwa mitundu ya anthu.
4Ku Ejipito kudzafika nkhondo,
ndipo ku Etiopiya kudzagwa mavuto.
Anthu ambiri adzaphedwa ku Ejipito,
chuma chake chidzatengedwa,
ndipo maziko ake adzagumuka.’
5“Etiopiya, Puti, Ludi, Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a m'dziko logwirizana naye, adzaphedwa nao limodzi pa nkhondoyo.
6“Zimene ndikunena Ine Chauta ndi izi:
Onse othandiza Ejipito adzaphedwa.
Ndipo kunyadira mphamvu zake kudzamthera.
Anthu ake adzaphedwa pa nkhondo
kuyambira ku Migidoli mpaka ku Siyene.
Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
7Dziko la Ejipito lidzasanduka bwinja
kupambana mabwinja onse opasuka.
Mizinda yake idzakhala yopasuka
kupambana mizinda ina yoonongeka.
8Nditamtentha Ejipito ndi kuthyola onse omuthandiza,
adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
9“Nthaŵi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopsa Aetiopiya, iwowo osadziŵako kanthu. Ndipo adzada nkhaŵa pa tsiku limene Ejipito adzaonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
10“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa:
Ndidzatuma Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni
kuti adzathetse chuma cha Ejipito.
11Iyeyo ndi anthu ake,
mtundu wa anthu ankhalwe kwambiri aja,
adzabwera kudzaononga dzikolo.
Adzasolola malupanga ao kuti amenyane ndi Aejipito,
ndipo dzikolo lidzadzaza ndi mitembo.
12Ndidzaumitsa mtsinje wa Nailo,
ndipo Ejipito ndidzamgulitsa kwa anthu oipa.
Dzikolo ndidzaliwononga, pamodzi ndi zonse zam'menemo,
polipereka m'manja mwa anthu akudza.
Ine Chauta ndatero.
13“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi:
Ndidzathetsa mafano
ndi kuwononga milungu yosema ya ku Memfisi.
Sikudzakhalanso mfumu ku Ejipito.
Ndipo ndidzaŵaopsa onse okhala m'dziko limenelo.
14“Mzinda wa Patirosi ndidzausandutsa chipululu.
Mzinda wa Zowani ndidzautentha.
Mzinda wa Thebesi ndidzaulanga.
15Mzinda wa Peluziumu, linga lolimba la Ejipito,
ndidzauthira mkwiyo wanga,
ndipo ndidzaononga gulu lankhondo la ku Thebesi.
16Ejipito yense ndidzamtentha,
ndipo Memfisi adzavutika kwambiri.
Malinga a ku Thebesi adzagumuka,
ndipo makoma ake adzaonongekeratu.
17Anyamata a ku Oni ndi a ku Pibeseti
adzaphedwa pa nkhondo,
ndipo akazi adzatengedwa ukapolo.
18Ku Tehafinehesi kudzachita mdima,
pamene ndidzathyole mphamvu za Ejipito kumeneko.
Motero kunyada kwake kudzatha.
Mitambo idzamuphimba,
ndipo okhala m'midzi yake adzatengedwa ukapolo.
19Motero ndidzamlanga Ejipito,
ndipo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Manja othyoka a mfumu ya ku Ejipito20Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti:
21“Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao, mfumu ya ku Ejipito. Ona, sadalimange kuti lichire, ndipo sadalilimbitse ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga.
22Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikudana naye Farao, mfumu ya ku Ejipito. Ndidzamthyola manja onse, lamoyo ndi lothyokalo, ndipo lupanga lake lidzamtayika.
23Ndidzaŵamwaza Aejipito pakati pa mitundu ya anthu ndi kuŵabalalitsira ku maiko ambiri.
24Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndipo m'manja mwake ndidzaikamo lupanga langa. Koma Farao ndidzamthyola manja, ndipo adzabuula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babiloniyo.
25Ndithu ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzafooka. Motero anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaika lupanga langa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pomenya nkhondo ndi dziko la Ejipito.
26Ndidzamwaza Aejipito pakati pa mitundu ya anthu, ndi kuŵabalalitsira ku maiko ambiri. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.