1 Ezek. 2.9, 10; Yes. 29.11 Pambuyo pake ndidaona buku m'dzanja lamanja la wokhala pa mpando wachifumu uja. Bukulo linali lolembedwa m'kati ndi kumbuyo komwe, ndipo linali lomatidwa ndi zimatiro zisanu ndi ziŵiri.
2Kenaka ndidaona mngelo wamphamvu akufunsa mokweza mau kuti, “Ndani ali woyenera kufutukula bukuli ndi kumatula zimatiro zake?”
3Koma panalibe ndi mmodzi yemwe Kumwamba, kapena pa dziko lapansi, kapena kunsi kwa dziko, wotha kufutukula bukulo kapena kuyang'anamo.
4Motero ndidalira kwambiri poona kuti sadapezeke woyenera kufutukula bukulo kapena kuyang'anamo.
5Gen. 49.9; Yes. 11.1, 10 Apo mmodzi mwa Akuluakulu aja adandiwuza kuti, “Usalire, pakuti Mkango wa m'fuko la Yuda, chidzukulu cha mfumu Davide, wapambana, ndipo Iye angathe kufutukula bukulo ndi kumatula zimatiro zake zisanu ndi ziŵiri zija.”
6 Yes. 53.7; Zek. 4.10 Tsono ndidaona Mwanawankhosa ataimirira pakati pa mpando wachifumu uja ndi Zamoyo zinai zija ndiponso Akuluakulu 24 aja. Mwanawankhosayo ankaoneka ngati wophedwa, ndipo anali ndi nyanga zisanu ndi ziŵiri ndiponso maso asanu ndi aŵiri. Masowo ndi Mizimu isanu ndi iŵiri ija ya Mulungu yotumidwa m'dziko lonse lapansi.
7Iyeyo adabwera nkulandira buku lija limene linali m'dzanja lamanja la wokhala pampando wachifumu uja.
8Mas. 141.2Pamene adalilandira, Zamoyo zinai zija, pamodzi ndi Akuluakulu 24 aja, zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosayo. Aliyense mwa Akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mikhate yagolide yodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a anthu a Mulungu.
9Mas. 33.3; 98.1; Yes. 42.10Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti:
“Ndinu oyenera kulandira bukuli
ndi kumatula zimatiro zake.
Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu
mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse,
a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.
10 Eks. 19.6; Chiv. 1.6 Mudaŵasandutsa mtundu wachifumu
ndi ansembe otumikira Mulungu wathu,
ndipo adzakhala olamulira pa dziko lapansi.”
11 Dan. 7.10 Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona namtindi wa angelo zikwizikwi pozungulira mpando wachifumu uja, Zamoyo zinai zija ndi Akuluakulu aja.
12Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti,
“Mwanawankhosa amene adaaphedwayu,
ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru,
nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.”
13Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti,
“Wokhala pa mpando wachifumu uja,
ndiponso Mwanawankhosa,
alandire chiyamiko, ulemu,
ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.”
14Apo Zamoyo zinai zija zidati, “Amen.” Ndipo Akuluakulu aja adadzigwetsa pansi moŵerama, napembedza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.