Chiv. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za m'mene amapembedzera Kumwamba

1Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona pakhomo potsekuka Kumwamba. Ndipo ndidamva wina akulankhula nane ndi liwu lomwe ndidaamva poyamba lija, limene linkamveka ngati kulira kwa lipenga. Adandiwuza kuti, “Bwera Kumwamba kuno, ndidzakuwonetse zimene ziyenera kuchitika bwino lino.”

2Ezek. 1.26-28; 10.1Nthaŵi yomweyo ndidagwidwa ndi Mzimu Woyera. Kumwambako ndidaona mpando wachifumu, wina atakhalapo pampandopo.

3Amene adaakhala pampandoyo, maonekedwe ake anali oŵala ngati miyala yoyera ndi yofiira, yonyezimira. Pozungulira mpando wachifumuwo panali utawaleza, maonekedwe ake ngati mwala woŵala, wobiriŵira.

4Pozungulira mpando wachifumu pomwepo panali mipando inanso 24 yachifumu, ndipo pamipandopo padaakhala Akuluakulu 24, atavala zovala zoyera, ali ndi zisoti zachifumu zagolide pamutu.

5Eks. 19.16; Tob. 12.15; Chiv. 8.5; 11.19; 16.18; Ezek. 1.13; Chiv. 1.4; Zek. 4.2Mu mpando wachifumu munkatuluka mphezi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando womwewo pankayaka miyuni isanu ndi iŵiri, ndiye kuti mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri.

6Ezek. 1.22

Ezek. 1.5-10; 10.14Patsogolo pake panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira.

Pakatimpakati, pozungulira mpando wachifumu uja, panali Zamoyo zinai, zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.

7Chamoyo choyamba chinkaoneka ngati mkango, chachiŵiri ngati ng'ombe, chachitatu chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo chachinai chinkaoneka ngati chiwombankhanga chouluka.

8Ezek. 1.18; 10.12; Yes. 6.2, 3Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo zinali ndi maso ponseponse ndi m'kati momwe. Usana ndi usiku zimaimba mosalekeza kuti,

“Ngoyera, ngoyera, ngoyera Ambuye,

Mulungu Mphambe,

amene analipo, amene alipo, amene alikudza.”

9Zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando wachifumuyu, amene ali ndi moyo wamuyaya.

10Pamene zikuchitika zimenezi, Akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pamaso pa wokhala pa mpando wachifumuyo, ndi kumpembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Ndipo amaponya pansi zisoti zao zaufumu patsogolo pa mpando wachifumuwo ndi kunena kuti,

11“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu,

ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu,

pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse.

Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help