Gen. 32 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yakobe akonzekera kukakumana ndi Esau

1Yakobe adanyamuka ulendo wake, ndipo angelo a Mulungu adakumana naye.

2Ataŵaona, adati, “Ili ndi gulu la ankhondo a Mulungu.” Motero malowo adaŵatcha Mahanaimu.

3Tsono Yakobe adatuma amithenga ake kwa Esau mbale wake ku Seiri, ku dziko la Edomu.

4Adaŵalangiza kuti akauze Esau kuti, “Ine Yakobe mtumiki wanu ndinkakhala kwa Labani, ndipo ndakhalitsako mpaka tsopano lino.

5Ndili ndi ng'ombe, abulu, nkhosa ndi mbuzi ndiponso akapolo ndi adzakazi. Ndikutumiza mau ameneŵa kwa inu mbuyanga, kuti mundikomere mtima!”

6Amithengawo atabwerera kwa Yakobe adati, “Tidapita kwa mbale wanu Esau, ndipo akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400 pamodzi.”

7Apo Yakobe adachita mantha kwambiri ndi kutaya mtima. Motero anthu amene anali nawo adaŵagaŵa m'magulu aŵiri, pamodzi ndi nkhosa, mbuzi, ng'ombe ndiponso ngamira.

8Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Esau akabwera, ndipo akachita nkhondo ndi gulu loyambali, gulu linalo lingathe kuthaŵa.”

9Pamenepo Yakobe adayamba kupemphera. Adati, “Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa bambo wanga Isaki, mundimve ine! Inu Chauta mudandiwuza kuti, ‘Bwerera ku dziko lako, dziko la abale ako, ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino.’

10Ine sindiyenera kulandira chifundo ndi chikhulupiriro chonse chimene mwandiwonetsa ine mtumiki wanu. Ndidaoloka Yordani ndilibe nkanthu komwe, koma ndodo yokha, koma tsopano ndabwerera ndi magulu aŵiri aŵa.

11Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa.

12

31Dzuŵa lidamtulukira Yakobe pamene ankachoka ku Penuwele, ndipo ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyung'unyu ija.

32Nchifukwa chake mpaka lero lino zidzukulu zonse za Israele sizidya nyama yapanyung'unyu, chifukwa ndi pa mtsempha wa panyung'unyu pomwe Yakobe adaamenyedwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help