1Tikukuthokozani Inu Mulungu,
ndithu tikukuthokozani.
Tikutchula dzina lanu mopemphera
ndipo tikulalika ntchito zanu zodabwitsa.
2Inu mukuti, “Pa nthaŵi imene ndiisankhule,
ndidzaweruza mwachilungamo.
3Pamene dziko lapansi likugwedezeka
pamodzi ndi zonse zokhalamo,
ndine amene ndimachirikiza mizati yake.”
4Ndimauza anthu odzitama kuti, “Musadzitame,”
ndiponso anthu oipa kuti,
“Musadzitukumule chifukwa cha mphamvu zanu.
5Musadzikuze chifukwa cha mphamvu zanu,
kapena kumalankhula zamwano.”
6Kugamula milandu sikuchokeratu kuvuma kapena kuzambwe,
ndiponso sikuchokera ku chipululu.
7Koma ndi Mulungu yekha amene amagamula milandu,
amatsitsa wina, nakweza wina.
8M'manja mwa Chauta mulitu chikho cha vinyo
wofanizira chilango chake,
vinyo wotutuma ndi wothirako dzoŵaŵa.
Adzatsanyula vinyoyo,
ndipo oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa,
nadzagugudiza mpaka ndungundungu zake.
9Koma ine sindidzaleka kukondwera,
ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobe
mpaka muyaya.
10Iye adzaphwanya mphamvu za anthu onse oipa,
koma adzaonjezera mphamvu za anthu okhulupirira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.