1
3Maliseche ako adzakhala poyera,
ndipo udzachita manyazi kwambiri.
Ndidzalipsira, ndipo palibe amene adzandiletsa.”
4Woyera uja wa Israele ndiye Mpulumutsi wathu,
dzina lake ndi Chauta Mphambe.
5Akuuza Babiloni kuti,
“Khala chete ndi kuloŵa mu mdima,
iwe namwali, Kaldeya.
Sadzakutchulanso mfumukazi ya maufumu.
6Ndidaŵakwiyira anthu anga,
ndidaŵanyoza ngati si anthu anga.
Ndidaŵapereka m'manja mwako,
ndipo iwe sudaŵachitire chifundo.
Udaumira mtima ndi nkhalamba zomwe.
7Unkaganiza kuti nthaŵi zonse
udzakhala mfumukazi,
mwakuti zinthu zimenezi sudazisamale,
sudaganizirenso m'mene zidzathere.”
8 Chiv. 18.7, 8 “Nchifukwa chake tsono umvetsere izi,
iwe wongokonda zokondweretsawe,
iwe amene umakhala pabwino,
numaganiza mumtima mwako kuti,
‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai.
Sindidzakhala konse wamasiye,
ndipo ana anga sadzafa.’ ”
9Koma m'kamphindi, tsiku limodzi,
zinthu ziŵiri zonsezi zidzakugwera.
Ana ako onse kukufera, iweyo kusanduka wamasiye,
zonsezo zidzakugwera pamodzi,
ngakhale kuti uli ndi matsenga ambiri
ndi zithumwa zamphamvu.
10“Sunkada nako nkhaŵa konse kuipa kwako,
unkaganiza kuti palibe wokupenya.
Kuchenjera kwako ndi nzeru zako zidakusokeza,
ndipo mumtima mwako unkaganiza kuti,
‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai.’ ”
11Tsoka lidzakugwera,
ndipo sudzatha kuliletsa ndi matsenga ako.
Chiwonongeko chidzakufikira, iwe osatha kuchithaŵa,
chipasupasu chosayembekezeka konse
chidzakugwera mwadzidzidzi.
12Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako.
Wakhala ukuzigwiritsa ntchito
chiyambire cha ubwana wako.
Mwina mwake zingakuthandize
kapena nkuwopsa nazo adani ako.
13Udangodzitopetsa nako kupempha
malangizo ambiri.
Nabwere okulangizawo kuti adzakupulumutse.
Abweretu anthu amene amaphunzira zakumlengalenga,
namayang'ana nyenyezi, amenenso amati
mwezi ukakhala nkumalosa zimene zidzakuchitikira.
14“Taona, anthuwo ali ngati mapesi,
adzapsa ndi moto.
Sangathe kudzipulumutsa
ku mphamvu ya malaŵi ake.
Moto wake si woti nkuwotha
kapena kusendera pafupi nawo ai.
15Ndimo m'mene adzakuthandizire anthuwo amene
wakhala ukugwira nao ntchito ndi kuchita nao
malonda chiyambire cha ubwana wako.
Onsewo adzangomwazikana,
sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.