1 Sam. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ansembe aphedwa.

1 Mas. 57; 142 Pamenepo Davide adathaŵa ku Gati, nakabisala ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi onse a m'banja la bambo wake atamva, adapita kumene kunali Davide.

2Tsono aliyense amene anali pa mavuto, kapena anali ndi ngongole, kapena anali wosakondwa, onsewo adasonkhana kwa Davide. Iyeyo ankaŵatsogolera. Onse anali ngati anthu 400 pamodzi.

3Pambuyo pake Davide adachoka kumeneko, napita ku Mizipa ku Mowabu. Adapempha mfumu ya ku Mowabu kuti, “Chonde, bwanji bambo wanga ndi mai wanga akhale nao kuno, mpaka nditadziŵa zimene Mulungu adzandichitire.”

4Choncho adaŵasiya kumeneko makolo akewo kwa mfumu ya ku Mowabuko, ndipo iwo adakhala komweko nthaŵi yonse imene Davide ankabisala kuphanga kuja.

5Tsono mneneri Gadi adauza Davide kuti, “Musakhale pano. Muchoke, mupite ku dziko la Yuda.” Pomwepo Davide adachoka, nakaloŵa m'nkhalango ya Hereti.

6Tsono Saulo adamva kuti Davide ndi anthu ake adapezeka. Tsiku limenelo Sauloyo adaakhala pansi patsinde pa mtengo wa mbwemba womera pa chitunda china ku Gibea, mkondo uli m'manja, ankhondo ake atamzungulira.

7Ndiye Sauloyo adafunsa ankhondo ake aja kuti, “Imvani tsono inu Abenjamini. Kodi mwana wa Yese adzakupatsani minda aliyense mwa inu? Kodi adzakusandutsani atsogoleri a magulu ankhondo nonsenu?

8Mwina nchifukwa chaketu mukundichita chiwembu chotere. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adandiwululira pamene mwana wanga ankagwirizana ndi mwana wa Yese. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akulabadako za ine kapena kundinong'onezako kuti mwana wanga wautsa mtima wa munthu wanga Davide kuti andiwukire, monga akuchitira leromu.”

9 1Sam. 21.7-9; Mas. 52 Apo Doegi Mwedomu, amene adaaimirira pafupi ndi nduna za Saulo, adanena kuti, “Ine ndidamuwona mwana wa Yese akupita ku Nobu kwa Ahimeleki, mwana wa Ahitubi.

10Ndipo Ahimelekiyo adafunsa Chauta zimene Davide ankayenera kuchita. Kenaka adampatsa chakudya, nampatsanso lupanga la Goliyati, Mfilisti uja.”

11Tsono mfumu Saulo adaitanitsa wansembe Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, pamodzi ndi onse a m'banja la bambo wake, amene anali ansembe ku Nobu. Onsewo adabwera kwa mfumu.

12Ndipo Saulo adati, “Imva tsono, iwe mwana wa Ahitubi.” Iye adayankha kuti, “Inde, mbuyanga.”

13Saulo adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wandichita chiwembu iwe ndi mwana wa Yese? Wampatsa buledi ndi lupanga, ndipo wamfunsira kwa Mulungu zoti achite. Taonani, tsopano wandiwukira, ndipo akundilalira lero lino!”

14Koma Ahimeleki adayankha mofunsa kuti, “Amfumu, kodi ndani pakati pa ankhondo anu amene ali wokhulupirika ngati Davide? Iye uja ndi mkamwini wanu, mtsogoleri wa gulu lanu lokutchinjirizani, ndiponso munthu wolemekezeka m'banja mwanu?

15Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu zoti achite? Iyai, amfumu! Musandinenere kanthu kena kalikonse koipa, ine mtumiki wanu, kapenanso wina aliyense wa m'banja la bambo wanga, pakuti sindikudziŵa kanthu pa nkhaniyi mpang'ono pomwe.”

16Komabe mfumu idati, “Iwe Ahimeleki, ndi onse a m'banja la bambo wako, mufa ndithu nonse!”

17Tsono idauza alonda omwe anali naye kuti, “Apheni ansembe a Chautaŵa, chifukwa akugwirizana ndi Davide. Adaadziŵa kuti Davideyo adathaŵa, koma sadandiwululire zimenezo.” Koma anyamata a mfumuwo sadasamule manja kuti aphe ansembe a Chauta.

18Pomwepo mfumu idauza Doegi kuti, “Kaŵaphe ndiwe.” Doegi, Mwedomu uja, adapitadi kukapha ansembewo. Adapha anthu 85 ololedwa kuvala efodi ya thonje lokoma.

19Kunena za Nobu, mzinda wa ansembe uja, Saulo adalamula kuti anthu onse okhalamo aphedwe. Choncho amuna ndi akazi, ana ndi makanda, kudzanso ng'ombe, abulu ndi nkhosa, zonsezo adazipha ankhondo ake.

20Koma mmodzi mwa ana aamuna a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake Abiyatara, adapulumuka, nathaŵa kutsatira Davide.

21Ndipo adauza Davide kuti Saulo adapha ansembe a Chauta.

22Davide adauza Abiyatara kuti “Ha! Tsiku limene lija nditaona kuti Doegi Mwedomu ali konkuja, ndidaadziŵa kuti kosapeneka konse akauza Saulo. Nchifukwa chake tsono uli pa ine mlandu wa imfa ya onse a m'banja la bambo wako.

23Koma iwe khala ndi ine, usaope ai, pakuti amene akufuna moyo wako, akufunanso moyo wanga. Ukakhala ndi ine, ukhala pabwino.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help