1Chaka cha 160, Aleksandro, mwana wa Antioko wotchedwa Epifane, adanyamuka nakalanda Ptolemaisi. Anthu akumeneko adamulandira bwino ndipo adamulonga ufumu, iye nkumalamulira.
2Mfumu Demetriyo atamva zimenezo, adasonkhanitsa gulu lankhondo lamphamvu, napita kukakumana naye kuti amenyane naye nkhondo.
3Nthaŵiyo Demetriyo adatumizira Yonatani kalata ndi mau amtendere ndi omutamanda kwambiri.
4Anali ndi maganizo akuti, “Tifulumire kupangana naye za mtendere, asanapangane ndi Aleksandro zakuti amthandize kumenyana nafe.”
5Demetriyo ankaopa kuti Yonatani adzakumbukira zoipa zonse zimene adaamchita iyeyo, abale ake ndi anthu a mtundu wake.
6Choncho adaloleza Yonatani kulemba asilikali ndi kupanga zida zankhondo ndi kukhala bwenzi lake, ndipo adalamula kuti amubwezere akaidi otsekeredwa m'boma lankhondo lija.
7Yonatani adapita ku Yerusalemu naŵerenga kalatayo pamaso pa anthu onse ndi pa ankhondo okhala m'boma lankhondo.
8Onse adachita mantha aakulu, atamva kuti mfumu wapatsa Yonatani chilolezo cha kulemba ankhondo.
9Anthu okhala m'boma lankhondowo adabwezera akaidi aja kwa Yonatani, ndipo iye adaŵapereka kwa abale ao.
10Yonatani adakhala ku Yerusalemu nayamba kumanganso ndi kukonza mzindawo.
11Adalamula antchito kutenga miyala yosema ndi kumanganso makoma ndi malinga ozinga phiri la Ziyoni, kuti aŵalimbitse, ndipo ntchitoyo idachitikadi.
12Tsono achilendo onse okhala m'malinga omangidwa ndi Bakide aja adathaŵa.
13Aliyense adasiya malo ake nabwerera ku dziko lakwao.
14Ku Betizure kokha kudaatsala ena opatukana ndi Malamulo, popeza kuti pa malo amenewo padaasanduka pothaŵira anthu ochimwa.
15Tsono mfumu Aleksandro adaazimva zonse zimene Demetriyo adaalonjeza kupatsa Yonatani. Anthu enanso adamfotokozera za nkhondo za Yonatani ndi za abale ake ndi za zochita zao zachamuna, ndiponso za zovuta zimene adazipirira.
16Apo Aleksandro adafunsa kuti, “Kodi tingapeze munthu wina aliyense wofanafana naye? Tsono tifulumire kuchita naye chibwenzi ndi kukhala ogwirizana naye.”
17Choncho adamtumizira kalata, mau ake anali otere:
18“Ndine, mfumu Aleksandro ndi kupereka moni kwa mbale wanga Yonatani.
19Tamva za inu kuti ndinu munthu wamphamvu ndi woyenera kukhala bwenzi lathu.
20Nchifukwa chake tikukusankhulani lero lomwe kuti mukhale mkulu wa ansembe onse pa mtundu wanu, ndipo tikukutchulani Bwenzi la Mfumu.” Tsono nthaŵi yomweyo adamtumizira mkanjo wofiirira ndi chisoti chaufumu chagolide. Ndipo adati, “Muzithandizana nafe, ndipo muchisunge chibwenzi chathuchi.”
21Yonatani adavala mkanjo waunsembe uja pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri wa chaka cha 160, pa tsiku la chikondwerero cha mahema. Ndipo adalemba magulu ena a asilikali, napanganso zida zambiri.
22Demetriyo atamva zimene zidaachitikazo, adamva chisoni.
23Adafunsa kuti, “Ife tachitapo chiyani pamenepa? Aleksandro wayamba ndiye kupalana chibwenzi ndi Ayuda, kuti alimbitse mphamvu zake?
24Inenso ndifuna kulemba mau oŵakopa ndi kuŵalonjeza ulemu ndi mphatso, kuti iwowo andipatse chithandizo chao.”
25Tsono adaŵalembera kalata yonena kuti,
“Ndine, mfumu Demetriyo, ndikukulonjerani inu mtundu wa Ayuda onse.
26Tamva m'mene mwasungira zimene mudapangana nafe ndi kulimbitsa chibwenzi chathu, osayanjana ndi adani athu. Ndipo ife takondwa nazo kwambiri.
27Tsopano musaleke kutikhulupirira. Tidzalipira ntchito zimene mukutigwirira pokupatsani zaufulu.
28Zoonadi, tikuchotserani misonkho yambiri, ndipo tidzakupatsani mphatso.
29Kuyambira lero, ndapatsa ufulu kwa Ayuda onse kuti asakhome msonkho wa mchere ndi misonkho inanso. Chigawo chachitatu cha dzinthu dza m'munda,
30, ndiponso za masiku atatu okonzekera ndi masiku atatu otsata chikondwerero chilichonse, kwa Ayuda onse okhala m'dziko langa masiku amenewo akhale masiku osakhoma msonkho ndi opezera ufulu.
35Pa masiku amenewo palibe ndi mmodzi yemwe adzathe kuŵakakamiza kubwezera ngongole, kapena kuŵavuta ndi mlandu wina uliwonse.
36Tidzaloŵetsa Ayuda m'gulu lankhondo la mfumu okwanira chiŵerengero cha 30,000, ndipo adzalandira malipiro omwe amalandira asilikali a mfumu.
37Ena mwa iwo adzaŵakhazikitsa m'malinga ankhondo aakulu a mfumu. Ena adzalandira ntchito zapamwamba zimene timapatsa anthu okhulupirika a m'dziko mwathu. Enanso adzakhala atsogoleri olamulira pa magulu ao ankhondo. Onse azidzatsata malamulo ao monga mfumu idalamulira m'dziko la Yudeya.
38“Zamadera atatu a ku Samariya oyandikana ndi Yudeya aja, maderawo adzakhala ophatikana ndi Yudeyayo, nkusanduka ngati dziko limodzi. Motero adzatsata mfumu imodzi, sadzamveranso wina, koma mkulu wa ansembe yekha.
39Ndapereka ngati mphatso ku Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu mzinda wa Ptolemaisi ndi midzi yake yozungulira, kuti papezekeko ndalama zofunikira pa chipembedzo.
40Ndipo ineyo chaka chilichonse ndidzapereka ndalama zasiliva 15,000. Adzazitapa pa msonkho wa mfumu ku malo oyenera.
41Ndalama zina zimene zidaayenera kuperekedwa kale, koma sadazipereke, zonsezo adzazipereka tsopano ku ntchito za ku Nyumba ya Mulungu.
42Ndipo ndalama zasiliva 5,000 zimene okhometsa msonkho anga ankasonkha chaka chilichonse pa zopereka zonse zimene anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Mulungu, sadzazitenganso ai, chifukwa ndi za ansembe ogwira ntchito komweko.
43Aliyense wothaŵira m'Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu kapena m'zipinda zake, chifukwa chosakhoma msonkho, kapena chifukwa cha ngongole ina iliyonse, adzakhala paufulu ndipo zabwino zonse zimene ali nazo m'dziko mwathu palibe munthu adzazikhudza.
44“Ndalama zofunika kuti amangire Nyumba ya Mulungu kapena kuikonza, adzazitapa pa msonkho wa mfumu.
45Ndalama zofunika kuti amangenso makoma a Yerusalemu ndi kulimbitsa malinga ake, ndiponso zofunika kuti amangenso malinga a mizinda ya ku Yudeya, zonsezo adzazitapanso pa msonkho wa mfumu.”
Yonatani akana mau a Demetriyo46Yonatani ndi anthu atamva mauwo, sadafune kuŵalandira ndi kuŵavomera, chifukwa adaakumbukira zoipa zazikulu zimene mfumu Demetriyo adaaŵachita Aisraele ndi misonkho yolemetsa imene adaaŵalamula.
47Iwo adasankhula kutsata Aleksandro amene anali woyamba kuŵauza anthu mau amtendere. Motero adakhala nthaŵi zonse ogwirizana nawo.
48Mfumu Aleksandro adasonkhanitsa magulu aakulu ankhondo, nakamanga zithando zake zankhondo kuyang'anana ndi za Demetriyo.
49Tsono mafumu aŵiriwo atayamba kumenyana nkhondo, ankhondo a Demetriyo adathaŵa, ndipo Aleksandro adaŵalondola naŵagonjetsa.
50Adamenya nkhondo ndi mphamvu mpaka dzuŵa kuloŵa, ndipo Demetriyo adaphedwa pa tsikulo.
Aleksandro alemekeza Yonatani51Aleksandro adatuma amithenga kwa Ptolemeyo, mfumu ya ku Ejipito, kukamuuza kuti,
52“Ndaloŵanso m'dziko langa ndipo ndakhalanso pa mpando waufumu wa makolo anga. Boma lili m'manja mwanga, dziko lonse ndikulamulira ndine.
53Demetriyo ndidamthira nkhondo, ndidamgonjetsa iyeyo ndi ankhondo ake, motero dziko lake ndidalanda.
54Ndiye inu tsopano tipalane chibwenzi. Mundipatse mwana wanu wamkazi kuti ndimkwatire. Ndidzakhala mkamwini wanu, ndipo ndidzakupatsani inu pamodzi ndi iyeyo mphatso zoyenerera ukulu wanu.”
55Mfumu Ptolemeyo adayankha kuti, “Nlodala tsiku limene mudabwereranso ku dziko la makolo anu ndi kukhala pa mpando wao waufumu.
56Tsopano ndidzakuchitirani zomwe mwalemba m'kalata mwanu. Koma bwerani tikumane ku Ptolemaisi, ndipo mudzakhaladi mkamwini wanga monga mwanenera.”
57Pa chaka cha 162 Ptolemeyo adanyamuka ku Ejipito, pamodzi ndi mwana wake wamkazi Kleopatra, kupita ku Ptolemaisi.
58Mfumu Aleksandro adabwera kudzakumana naye Ptolemeyo, ndipo Ptolemeyoyo adampatsa mwana wake wamkazi Kleopatra. Adachita madyerero aukwati ku Ptolemaisi pa chaka cha 162 ndi ulemu waukulu, monga chinaliri chizoloŵezi cha mafumu.
59Mfumu Aleksandro adalembanso ina kalata kwa Yonatani yomuitana.
60Yonatani adanka ndi ulemu ku Ptolemaisi, kumeneko adaonana nawo mafumu aŵiriwo. Adapereka kwa iwo ndi kwa abwenzi ao siliva ndi golide ndi mphatso zina zambiri, motero adapeza kuyanja pamaso pao.
61Nthaŵi yomweyo anthu ena oipa a ku Israele adadza kwa mfumu kuti amneneze. Koma mfumu sidalabadeko za iwowo.
62Mfumu idalamula kuti amuvule Yonatani zovala zake ndi kumuveka zovala zofiirira. Adaterodi.
63Tsono mfumu idamkhazika pa mpando pafupi naye, nkuuza nduna zake kuti, “Pita nayeni pakatikati pa mzinda, muzikalengeza kuti pasapezeke munthu ndi mmodzi yemwe wodzamneneza pa nkhani iliyonse, pasapezekenso wina womuvuta.”
64Omneneza aja atangoona ulemu umene Yonatani adaaulandira, potsata zolengeza zija, nkuwonanso zovala zofiirira zija zili m'thupi, adathaŵa.
65Mfumu idaonjeza pa ulemuwo pakumuika m'gulu la abwenzi ake apamtima, ndipo adamsankha kuti akhale mtsogoleri wamkulu wa ankhondo ndiponso bwanamkubwa m'chigawo chake.
66Yonatani adabwerera ku Yerusalemu ali ndi mtendere ndi chimwemwe.
Yonatani agonjetsa Apoloniyo67Chaka cha 165, Demetriyo wachiŵiri, mwana wa Demetriyo woyamba, adanyamuka ku Krete, nabwera ku dziko la makolo ake.
68Atamva zimenezo, mfumu Aleksandro adavutika mu mtima, nabwerera ku Antiokeya.
69Demetriyo adakhazika Apoloniyo kuti akhale bwanamkubwa wa Celesiriya. Apoloniyoyo adasonkhanitsa gulu lalikulu lankhondo, nadzamanga zithando zake zankhondo pafupi ndi Yaminiya. Adatumizira Yonatani mau akuti,
70“Ndiwe wekhatu amene ukutichita ife chiwembu, ndipo ine ndasanduka wosekedwa ndi wonyozedwa chifukwa cha iwe. Chifukwa chiyani ukutiwukirabe, pamene uli wekhawekha kumapiri kuno?
71Tsopano ngati ukukhulupirira mphamvu zakozo, tsika kumeneko, udzakumane nane kuchigwa kuno, tidzayesane, chifukwa ine ndili ndi ankhondo a ku mizinda.
72Ufunse kuti udziŵe za ine ndi za enawo amene amatithandiza. Anthuwo adzakuuza kuti sungathe kulimbana nafe, popeza kuti makolo ako tidaŵagonjetsa kaŵiri kudziko kwao komwe.
73Ndiye kuti sudzatha kulimbana ndi asilikali anga okwera pa akavalo ndi asilikali ena ambirimbiri oyenda pansi, ku chigwa kuno kumene kulibe matanthwe kapena miyala kapena malo ena aliwonse othaŵirako.”
74Yonatani atamva mau a Apoloniyoyo, adapsa mtima kwabasi. Adasankhula anthu 10,000 nanyamuka ku Yerusalemu. Mbale wake Simoni adabwera kudzamthandiza.
75Adamanga zithando zankhondo pafupi ndi Yopa. Koma anthu akumeneko adaŵatsekera zipata za mzinda, chifukwa kumeneko kunali kaboma kankhondo ka Apoloniyo. Tsono Yonatani adayamba kumenyana nawo nkhondo.
76Anthu amumzindamo adachita mantha natsekula zipata, ndipo Yonatani adalanda Yopa.
77Pakumva zimenezo, Apoloniyo adatenga ankhondo okwera pa akavalo 3,000 ndi gulu lalikulu la ankhondo ena, napita ku Azoto, kuchita ngati kungoyenda chabe. Nthaŵi yomweyo adasendera ku chigwa, chifukwa ankakhulupirira kuchuluka kwa asilikali ake okwera pa akavalo.
78Tsono Yonatani adamtsata mpaka ku Azoto, kumeneko magulu aŵiri a asilikali adamenyana nkhondo.
79Apoloniyo adasiya kumbuyo kwao asilikali okwera pa akavalo 1,000 atabisala.
80Koma Yonatani adaazindikira kuti kuli obisalira kumbuyo kwake, chifukwa ankhondowo adaazinga gulu lake lankhondo nkumalasa anthu ake ndi mivi yao kuyambira m'maŵa mpaka madzulo.
81Koma anthu ake adalimbika, monga m'mene Yonatani adaaŵalamulira, ndipo akavalo a adani adayamba kutopa.
82Tsono Simoni adabwera ndi gulu lake, namenyana nkhondo ndi gulu lalikulu lija la adani, chifukwa akavalo anali atatopa kwambiri. Adaniwo poona kuti zathina, adathaŵa.
83Ankhondo aja a pa akavalo adangoti balala m'chigwa, ndipo othaŵawo adakafika ku Azoto, kumene adakaloŵa m'Bete-Dagoni, nyumba ya fano lao, kuti apulumukiremo.
84Yonatani adatentha mzinda wa Azoto ndi mizinda yozungulira, nafunkha chuma chake. Adatenthanso nyumba yopembedzeramo Dagoni ndi onse amene adaathaŵiramo.
85Anthu onse amene adaŵapha pa nkhondo ndi ena ochita kuŵatentha, adakwanira 8,000.
86Yonatani adachokako, nadzamanga zithando zake zankhondo pafupi ndi Askaloni. Anthu akumeneko adatuluka kudzakumana naye, ndipo adamchitira ulemu waukulu.
87Tsono Yonatani adabwerera ku Yerusalemu ndi anthu ake ndi chuma chambiri chimene adaachifunkha.
88Mfumu Aleksandro atamva zimene zidachitikazo, adapatsa Yonatani ulemu wina.
89Adamtumizira bakolo yagolide yomangira nsalu, potsata mwambo wokhalira abale a mfumu okha, nampatsa mzinda wa Ekeroni ndi midzi yake yonse kuti ikhale yake.
Kufa kwa AleksandroWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.