1 Mbi. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ana a mfumu Davide

1Naŵa ana a Davide amene adabadwira ku Hebroni. Amoni ndiye mwana wake wachisamba, mai wake anali Ahinowamu, wa ku Yezireele. Daniele ndiye mwana wake wachiŵiri, mai wake anali Abigaile, wa ku Karimele.

2Mwana wake wachitatu ndi Abisalomu, mai wake anali Maaka, mwana wa Talimai, mfumu ya ku Gesuri. Mwana wake wachinai ndi Adoniya, mai wake anali Hagiti.

3Mwana wake wachisanu ndi Sefatiya, mai wake anali Abitala. Mwana wake wachisanu ndi chimodzi ndi Itireamu, mai wake anali Egila.

4 mwana wa Amiyele.

6Panalinso ana aŵa: Ibara, Elisama, Elifeleti,

7Noga, Nefegi, Yafia,

8Elisama, Eliyada ndi Elifeleti, ana asanu ndi anai.

9Onseŵa anali ana a Davide, osaŵerengera ana a azikazi ake. Mlongo wao anali Tamara.

Zidzukulu za mfumu Solomoni

10Nazi zidzukulu za Solomoni: Rehobowamu adabereka Abiya, Abiya adabereka Asa, Asa adabereka Yehosafati,

11Yehosafati adabereka Yoramu. Yoramu adabereka Ahaziya, Ahaziya adabereka Yowasi.

12Yowasi adabereka Amaziya, Amaziya adabereka Azariya, Azariya adabereka Yotamu.

13Yotamu adabereka Ahazi, Ahazi adabereka Hezekiya, Hezekiya adabereka Manase.

14Manase adabereka Amoni, Amoni adabereka Yosiya.

15Ana a Yosiya naŵa: Yohanani, mwana wake wachisamba. Wachiŵiri anali Yehoyakimu, wachitatu anali Zedekiya ndipo wachinai anali Salumu.

16Ana aamuna a Yehoyakimu anali aŵa: Yekoniya ndi Zedekiya.

Zidzukulu za Yehoyakimu

17Ana a Yekoniya, wam'ndende uja, naŵa: Sealatiele,

18Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama, ndiponso Nedabiya.

19Ana a Pedaya naŵa: Zerubabele ndi Simei. Ana a Zerubabele naŵa: Mesulamu, Hananiya, ndi Selomiti mlongo wao.

20Panalinso Asuba, Owele, Berekiya, Hasadiya ndi Yusabusede, asanu pamodzi.

21Ana a Hananiya naŵa: Pelatiya, Yesaya, Refaya, Arinani, Obadiya ndi Sekaniya.

22Mwana wa Sekaniya anali Semaya. Ana a Semaya naŵa: Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati, asanu ndi mmodzi.

23Ana a Neariya, naŵa: Eliyoenai, Hizikiya ndi Azirikamu, atatu.

24Ana a Eliyoenai, naŵa: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya ndi Anani, asanu ndi aŵiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help