1Tsono Yobe adayankha kuti,
2“Iwe, kodi wandithandiza ine
munthu wosauka ndi wofookane ngati?
3Kodi wandilangiza zabwino ine,
munthu wopanda nzerune ngati?
Kodi wandiwuza nzeru zambiri pamenepa ngati?
4Kodi ndani adzamva mau akoŵa?
Nanga udazitenga kuti zonsezi?
5“Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa nthaka,
zonse zokhala m'madzi pansipo zikuvutika.
6Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu,
ndipo kumeneko sikuphimbika kwa Iye.
7Mulungu adayala thambo lakumpoto pa phompho,
adakoloŵeka dziko lapansi m'malo mwake,
pamene panali popanda nkanthu komwe.
8Amasunga madzi ambiri m'mitambo yochindikira,
koma mitamboyo sing'ambika.
9Amaphimba mwezi,
amauphimba ndi mtambo wake.
10Madzi Mulungu adaŵalembera malire onga uta,
motero adalekanitsa kuŵala ndi mdima.
11Mizati yochirikiza thambo lakumwamba
imanjenjemera ndi mantha,
imazizwa pakumva kudzudzula kwa Mulungu.
12Ndi mphamvu zake adatontholetsa nyanja,
ndi nzeru zake adakantha chilombo cham'madzi chija
cha Rahabu.
13Ndi mpweya mwake adayeretsa zamumlengalenga,
ndi dzanja lake adapha chinjoka chothaŵa chija.
14Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake.
Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona.
Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.