Lev. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aroni apereka nsembe

1Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, Mose adaitana Aroni, ana ake ndi atsogoleri a Aisraele.

2Adauza Aroniyo kuti, “Utenge mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezo zikhale zopanda chilema, ndipo uzipereke pamaso pa Chauta.

3Tsono uuze Aisraele kuti, ‘Tengani tonde kuti muperekere nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwanawang'ombe ndi mwanawankhosa. Aŵiri onsewo akhale a chaka chimodzi, opanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza.

4Mutengenso ng'ombe ndi nkhosa kuti zikhale nsembe zachiyanjano zoti aziphere pamaso pa Chauta. Mubwerenso ndi zopereka za zakudya zosakaniza ndi mafuta, pakuti lero Chauta akuwonekerani.’ ”

5Zonse zimene Mose adalamula anthuwo, iwo adabwera nazo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Ndipo mpingo wonse udasendera pafupi, nupembedza Chauta.

6Apo Mose adati, “Nazi zimene Chauta akukulamulani kuti muchite, kuti ulemerero wake ukuwonekereni.”

7Ahe. 7.27 Pamenepo Moseyo adauza Aroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa, ndipo upereke nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kuti uchite mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a Aisraele. Ubwere ndi zopereka za anthuwo ndipo uchite mwambo wopepesera machimo ao, monga momwe Chauta walamulira.”

8Choncho Aroni adasendera pafupi ndi guwa, napha mwanawang'ombe woperekera nsembe yopepesera machimo, nsembeyo ya iye mwini wake.

9Ndipo ana ake adapereka magazi kwa Aroni. Iyeyo adaviika chala chake m'magazimo, naŵapaka pa nyanga za guwa, nathira magaziwo patsinde pa guwa lomwelo.

10Koma mafuta ndi imso, pamodzi ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, za nsembe yopepesera machimoyo, adazitenthera pa guwa, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

11Nyama yake ndi chikopa chake, adazitenthera kunja kwake kwa mahema.

12Tsono adapha nyama ya nsembe yopsereza, ndipo ana ake a Aroniyo atampatsira magazi, iye adawaza magaziwo pa guwa molizungulira.

13Pambuyo pake adampatsira nyama ya nsembe yopsereza yoduladula, pamodzi ndi mutu wake womwe, ndipo iye adazitentha pa guwa.

14Kenaka atatsuka matumbo ndi miyendo, adazitentha paguwa pomwepo, pamodzi ndi nsembe yopsereza ija.

15Tsono adapereka zopereka za anthuwo, natenga mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthuwo, naipha nkuipereka ngati nsembe yopepesera machimo, monga adachitira ndi nsembe yopepesera machimo yoyambayo.

16Apo adabwera ndi nsembe yopsereza, naipereka potsata mwambo wake.

17Adaperekanso chopereka cha chakudya, natapako ufawo dzanja limodzi nautentha pa guwa, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yam'maŵayo.

18 Lev. 3.1-11 Tsono adaphanso ng'ombe ndi nkhosa yamphongo, kuperekera anthu nsembe yachiyanjano. Pambuyo pake ana a Aroni adampatsira magazi, ndipo iye adathira magaziwo pa guwa molizungulira.

19Adampatsiranso mafuta ang'ombe ndi mafuta a nkhosa yamphongo, mchira wamafuta, mafuta okuta matumbo, imso pamodzi ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi.

20Anawo adaika mafuta pa nganga, ndipo Aroni adatentha mafutawo pa guwa.

21Koma Aroni adaweyula ngangazo ndi ntchafu ya ku dzanja lamanja, kuti zikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta, monga momwe Mose adaalamulira.

22 Num. 6.22-26 Tsono Aroni adakweza manja ake pa Aisraele naŵadalitsa. Ndipo adatsika paguwa, pomwe adaperekera nsembe yopepesera machimo, nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano.

23Pamenepo Mose pamodzi ndi Aroni adakaloŵa m'chihema chamsonkhano. Atatulukamo, adadalitsa anthu aja, ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera anthu onsewo.

24Pompo moto udatuluka pamaso pa Chauta nupserezeratu nsembe yopsereza ndi mafuta omwe, zimene zinali paguwapo. Ndipo anthu ataona motowo, adafuula naŵeramitsa nkhope zao pansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help