Mas. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lakuti mfumu ipambane pa nkhondoKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto.

Mulungu wa Yakobe akuteteze.

2Akutumizire chithandizo kuchokera ku malo ake oyera,

akuchirikize kuchokera ku Ziyoni.

3Alandire zopereka zako zonse,

akondwere ndi nsembe zako zopsereza.

4Akupatse zimene mtima wako ukukhumba,

akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.

5Choncho tifuule ndi chimwemwe

chifukwa chakuti mwapambana pa nkhondo,

tikweze mbendera kutamanda dzina la Mulungu wathu.

Chauta akupatse zonse zimene wapempha.

6Tsopano ndikudziƔa

kuti Chauta adzathandiza wodzozedwa wake.

Adzamuyankha ali ku malo ake oyera kumwamba,

pakumpambanitsa kwathunthu ndi dzanja lake lamanja.

7Ena amatamira magaleta ankhondo,

ena amadalira akavalo,

koma ife timatamira dzina la Chauta, Mulungu wathu,

timamutama Iyeyo mopemba.

8Adani adzaphofomoka ndi kugwa,

koma ife tidzadzuka kukhala chilili.

9Inu Chauta, thandizani mfumu kuti ipambane.

Mutiyankhe pamene tikuitana.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help